YEREMIYA 27 - Buku Lopatulika Bible 2014

Yeremiya awachenjeza agonje kwa mfumu ya ku Babiloni

1Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,

2Yer. 28.10Yehova atero kwa ine: Udzipangire zomangira ndi magoli, nuziike pakhosi pako;

3nuzitumize kwa mfumu ya Edomu, ndi kwa mfumu ya Mowabu, ndi kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kwa mfumu ya Tiro, ndi kwa mfumu ya Sidoni, ndi dzanja la amithenga amene afika ku Yerusalemu kwa Zedekiya mfumu ya Yuda;

4nuwauze iwo anene kwa ambuyao, kuti, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Muzitero kwa ambuyanu:

5Mas. 115.15-16Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikulu ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.

6Yer. 28.14Tsopano ndapereka maiko onse awa m'manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga; ndiponso nyama za kuthengo ndampatsa iye kuti zimtumikire.

72Mbi. 36.20-21Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu akulu adzamuyesa iye mtumiki wao.

8Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake.

9Koma inu, musamvere aneneri anu, kapena akuombeza anu, kapena maloto anu, kapena alauli anu, kapena obwebweta anu, Musadzatumikira mfumu ya ku Babiloni;

10Yer. 27.14kakuti iwo akunenerani inu zonama, kuti akuchotseni inu m'dziko lanu, kunka kutali kuti ndikupirikitseni inu, ndipo inu mudzathedwa.

11Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m'dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo.

12Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m'goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye ndi anthu ake, ndipo mudzakhala ndi moyo.

13Ezk. 18.31Mudzaferanji, iwe ndi anthu anu, ndi lupanga ndi njala, ndi chaola, monga wanena Yehova za mtundu umene ukana kumtumikira mfumu ya ku Babiloni?

14Yer. 27.10Musamvere mau a aneneri amene anena ndi inu, kuti, simudzamtumikira mfumu ya ku Babiloni; pakuti akunenerani zonama.

15Yer. 27.10Pakuti sindinawauma iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupirikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.

162Mbi. 36.7, 10Ndiponso ndinanena kwa ansembe ndi kwa anthu onsewa, kuti, Yehova atero: Musamvere mau a aneneri anu amene akunenerani inu, kuti, Taonani, zipangizo za nyumba ya Yehova zidzatengedwanso ku Babiloni posachedwa; pakuti akunenerani inu zonama.

17Musamvere amenewa; mtumikireni mfumu ya ku Babiloni, ndipo mudzakhala ndi moyo; chifukwa chanji mudzi uwu udzakhala bwinja?

18Koma ngati ndiwo aneneri, ndipo ngati mau a Yehova ali ndi iwo, tsopano apembedzere Yehova wa makamu, kuti zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu, zisanke ku Babiloni.

192Maf. 25.13-17Pakuti Yehova wa makamu atero, za zoimiritsa, ndi za thawale, ndi za zoikirapo, ndi za zipangizo zotsala m'mudzi uwu,

202Maf. 24.14-15zimene sanazitenge Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, pamene anamtenga ndende Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Babiloni; ndi akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu;

21inde, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu;

222Maf. 25.13; 2Mbi. 36.21-22; Ezr. 1.7-8adzanka nazo ku Babiloni, kumeneko zidzakhala, mpaka tsiku limene ndidzayang'anira iwo, ati Yehova; pamenepo ndidzazikweza, ndi kuzibwezera kumalo kuno.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help