EZEKIELE 20 - Buku Lopatulika Bible 2014

Machimo a Aisraele chitulukire iwo m'dziko la Ejipito

1 Ezk. 14.1 Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chiwiri, mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, anadza akulu ena a Israele kufunsira kwa Yehova, nakhala pansi iwowa pamaso panga.

2Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

3Ezk. 14.3Wobadwa ndi munthu iwe lankhula ndi akulu a Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwadza kodi kufunsira kwa Ine? Pali Ine, sindidzafunsidwa ndi inu, ati Ambuye Yehova.

4Ezk. 16.2Udzawaweruza kodi, wobadwa ndi munthu iwe? Udzawaweruza? Uwadziwitse zonyansa za makolo ao,

5Eks. 4.31; 6.7; 20.2nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija ndinamsankha Israele, ndi kukwezera mbeu ya nyumba ya Yakobo dzanja langa, ndi kudzidziwitsa kwa iwo m'dziko la Ejipito, pakuwakwezera dzanja langa, ndi kuti, Ine ndine Yehova Mulungu wanu;

6Eks. 3.8, 17tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, kunka nao kudziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;

7Yos. 24.14ndipo ndinanena nao, Aliyense ataye zonyansa za pamaso pake, nimusadzidetsa ndi mafano a Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

8Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito.

9Deut. 9.28Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito.

10Eks. 13.18Momwemo ndinatuluka nao m'dziko la Ejipito, ndi kulowa nao kuchipululu.

11Deut. 4.8; Aro. 10.5Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo.

12Eks. 20.8-11Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.

13Num. 14.22; Aro. 10.5Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha.

14Ezk. 20.9-22Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawatulutsa pamaso pao.

15Ndipo ndinawakwezeranso dzanja langa m'chipululu, kusawalowetsa m'dzikolo ndidawapatsa, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;

16Num. 15.39popeza ananyoza maweruzo anga, osayenda m'malemba anga, naipsa masabata anga; pakuti mitima yao inatsata mafano ao.

17Mas. 78.38Koma diso langa lidawaleka osawaononga, sindinawatha onse m'chipululu.

18Ndipo ndinati kwa ana ao m'chipululu, Musamayenda m'malemba a atate anu, musawasunga maweruzo ao, kapena kudzidetsa ndi mafano ao;

19Ine ndine Yehova Mulungu wanu, muziyenda m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita;

20Yer. 17.22muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala chizindikiro pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

21Ezk. 20.11, 13Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu.

22Ezk. 20.9, 14Koma ndinabweza dzanja langa ndi kuchichita, chifukwa cha dzina langa; kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu, amene ndinawatulutsa pamaso pao.

23Deut. 28.64Ndinawakwezeranso dzanja langa m'chipululu, kuti ndidzawabalalitsa mwa amitundu, ndi kuwamwaza m'maiko;

24popeza sanachite maweruzo anga, koma ananyoza malemba anga, naipsa masabata anga, ndi maso ao anatsata mafano a atate ao.

25Aro. 1.24Momwemonso ndinawapatsa malemba amene sanali abwino, ndi maweruzo osakhala nao ndi moyo;

26ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.

27Chifukwa chake wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi nyumba ya Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwa ichinso atate anu anandichitira mwano pakundilakwira Ine.

28Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.

29Pamenepo ndinanena nao, Msanje wotani uwu mumapitako? Momwemo dzina lake litchedwa Msanje, mpaka lero lino.

30Chifukwa chake uziti kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Mudzidetsa kodi monga umo anachitira makolo anu? Muchita chigololo kodi kutsata zonyansa zao?

31Ezk. 20.3Ndipo popereka zopereka zanu popititsa ana anu pamoto, mudzidetsa kodi ndi mafano anu onse mpaka lero lino? Ndipo kodi ndidzafunsidwa ndi inu, nyumba ya Israele? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindidzafunsidwa ndi inu;

32ndi ichi chimauka mumtima mwanu sichidzachitika, umo mukuti, Tidzakhala ngati amitundu, ngati mabanja a m'maiko, kutumikira mtengo ndi mwala.

Mulungu adzabweza Israele kuchokera kubalalikidwa iwo

33Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa, ndidzakhala mfumu yanu.

34Ndipo ndidzakutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani m'maiko munabalalikamo ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa.

35Yer. 2.35Ndipo ndidzalowa nanu m'chipululu cha mitundu ya anthu, ndi kukuweruzani komweko popenyana maso.

36Monga ndinaweruza makolo anu m'chipululu cha dziko la Ejipito, momwemo ndidzaweruza inu, ati Ambuye Yehova.

37Lev. 27.32Ndipo ndidzakupititsani pansi pa ndodo ya mbusa ndi kukulowetsani m'chimango cha chipangano;

38Mat. 25.32-33ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawatulutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israele; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

39Ower. 10.14; Yes. 1.13Ndipo inu, nyumba ya Israele, atero Ambuye Yehova, mukani, tumikirani yense mafano ake, ndi m'tsogolo momwe, popeza simundimvera Ine; koma musaipsanso dzina langa lopatulika ndi zopereka zanu ndi mafano anu.

40Yes. 56.7; 60.7; Aro. 12.1Pakuti pa phiri langa lopatulika, pa phiri lothuvuka la Israele, ati Ambuye Yehova, pomwepo onse a nyumba ya Israele, onsewo adzanditumikira Ine m'dzikomo; pomwepo ndidzawalandira, ndi pomwepo ndidzafuna nsembe zanu zokweza, ndi zoyamba za msonkho wanu, pamodzi ndi zopatulika zanu zonse.

41Ezk. 36.23; Aef. 5.2; Afi. 4.18Ngati fungo lokoma ndidzakulandirani pakukutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukuchotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.

42Ezk. 34.13Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakukulowetsani Ine m'dziko la Israele, m'dzikoli ndinalikwezera dzanja langa kulipereka kwa makolo anu.

43Ezk. 6.9Ndi pomwepo mudzakumbukira njira zanu, ndi zonse mudazichita ndi kudzidetsa nazo, ndipo mudzakhala onyansa pamaso pa inu nokha, chifukwa cha zoipa zanu zonse mudazichita.

44Ezk. 36.22M'mwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova nditachita nanu chifukwa cha dzina langa, si monga mwa njira zanu zoipa, kapena monga mwa machitidwe anu ovunda, nyumba ya Israele inu, ati Ambuye Yehova.

45Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

46Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako njira ya kumwera, nubenthulire mau kumwera, nunenere nkhalango ya kuthengo la kumwera kwa Yuda;

47nuziti kwa nkhalango ya kumwera kwa Yuda, Tamvera mau a Yehova, Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzayatsa moto mwa iwe, udzanyeketsa mtengo uliwonse wauwisi mwa iwe, ndi mtengo uliwonse wouma; malawi amoto sadzazimika, ndi nkhope zonse kuyambira kumwera kufikira kumpoto zidzapsa nao.

48Ndi anthu onse adzaona kuti Ine Yehova ndinauyatsa, sudzazimika.

49Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Anandinena, Wonena mafanizo uyu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help