1 AKORINTO 2 - Buku Lopatulika Bible 2014

Ulalikidwe wa Paulo

1 1Ako. 1.17 Ndipo ine, abale, m'mene ndinadza kwa inu, sindinadza ndi kuposa kwa mau, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu chinsinsi cha Mulungu.

2Agal. 6.14Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu, koma Yesu Khristu, ndi Iye wopachikidwa.

32Ako. 10.1, 10Ndipo ine ndinakhala nanu mofooka ndi m'mantha, ndi monthunthumira mwambiri.

4Aro. 15.19; 1Ako. 1.17Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu;

52Ako. 4.7kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.

6 1Ako. 1.20; Aef. 4.13 Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi yino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi yino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;

7Aef. 3.5, 9koma tilankhula nzeru ya Mulungu m'chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu,

8Luk. 23.34imene saidziwa mmodzi wa akulu a nthawi ya pansi pano: pakuti akadadziwa sakadapachika Mbuye wa ulemerero;

9Yes. 64.4koma monga kulembedwa,

Zimene diso silinaziona, ndi khutu silinazimva,

nisizinalowa mu mtima wa munthu,

zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.

10 1Pet. 4.11 Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.

11Aro. 11.33-34Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.

12Aro. 8.15Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.

131Ako. 1.17Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.

14Mat. 16.23; Aro. 8.5-7Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.

151Yoh. 4.1Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi mmodzi yense.

16Yes. 40.13; Yoh. 15.15Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize Iye? Koma ife tili nao mtima wa Khristu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help