EZEKIELE 37 - Buku Lopatulika Bible 2014

Masomphenya a mafupa

1 Luk. 4.1 Dzanja la Yehova linandikhalira, ndipo anatuluka nane mu mzimu wa Yehova, nandiika m'kati mwa chigwa, ndicho chodzala ndi mafupa;

2ndipo anandipititsa pamenepo pozungulira ponse, ndipo taonani, anali aunyinji pachigwa pansi, ndipo anaumitsitsa.

3Yoh. 5.21; Aro. 4.17Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, mafupa awa nkukhala ndi moyo kodi? Ndipo ndinati, Ambuye Yehova, mudziwa ndinu.

4Pamenepo anati kwa ine, Nenera kwa mafupa awa, nuti nao, Mafupa ouma inu, imvani mau a Yehova.

5Mas. 104.30Atero Ambuye Yehova kwa mafupa awa, Taonani, ndidzalonga mpweya mwa inu, ndipo mudzakhala ndi moyo.

6Ndipo ndidzakuikirani mtsempha, ndi kufikitsira inu mnofu, ndi kukuta inu ndi khungu, ndi kulonga mpweya mwa inu; ndipo mudzakhala ndi moyo; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

7M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndipo ponenera ine panali phokoso; ndipo taonani, panali gobedegobede, ndi mafupa anasendererana, fupa kutsata fupa linzake.

8Ndipo ndinapenya, taonani, panali mitsempha pa iwo, panadzaponso mnofu, ndi khungu linawakuta pamwamba pake; koma munalibe mpweya mwa iwo.

9Mas. 104.30Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kuchokera kumphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.

10Chiv. 11.11M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndi mpweya unawalowa, ndipo anakhala ndi moyo, naimirira chilili, gulu la nkhondo lalikulukulu ndithu.

11Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israele; taonani, akuti, Mafupa athu auma, chiyembekezo chathu chatayika, talikhidwa.

12Hos. 13.14Chifukwa chake, nenera, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani anthu anga, ndidzatsegula kumanda kwanu, ndi kukweza inu mutuluke m'manda mwanu, ndipo ndidzakulowetsani m'dziko la Israele.

13Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova potsegula Ine kumanda kwanu, ndi kukweza inu kukutulutsani m'manda mwanu, anthu anga inu.

14Ezk. 36.27Ndipo ndidzalonga mzimu wanga mwa inu, nimudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzakukhazikani m'dziko mwanu; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena ndi kuchichita, ati Yehova.

15Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

16Num. 17.2Tsono, iwe wobadwa ndi munthu, Tenga mtengo umodzi, nulembepo, Wa Yuda ndi wa ana a Israele anzake; nutenge mtengo wina, nulembepo, Wa Yosefe, mtengo wa Efuremu, ndi wa nyumba yonse ya Israele anzake;

17Ezk. 37.22, 24nuiphatikize wina ndi unzake ikhale mtengo umodzi m'dzanja lako.

18Ndipo ana a anthu a mtundu wako akanena ndi iwe, ndi kuti, Sutifotokozera nanga zitani izi?

19Ezk. 37.16-17Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga mtengo wa Yosefe uli m'dzanja la Efuremu, ndi wa mafuko a Israele anzake, ndi kuwaika pamodzi ndi mtengo wa Yuda, ndi kuiyesa mtengo umodzi; ndipo idzakhala umodzi m'dzanja langa.

20Ndipo mitengo imene ulembapo idzakhala m'dzanja mwako pamaso pao.

21Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israele pakati pa amitundu kumene adamkako, ndi kuwasokolotsa kumbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;

22Hos. 1.11; Yoh. 10.16ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israele; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.

23Ezk. 36.25-29Ndipo sadzadzidetsanso ndi mafano ao, kapena ndi zonyansa zao, kapena ndi zolakwa zao zilizonse; koma ndidzawapulumutsa mokhala mwao monse m'mene anachimwamo, ndi kuwayeretsa; m'mwemo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.

24Yes. 40.11; Ezk. 37.22; Luk. 1.32Ndi mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, ndipo iwo onse adzakhala ndi mbusa mmodzi, adzayendanso m'maweruzo anga, nadzasunga malemba anga ndi kuwachita.

25Ezk. 36.28Ndipo adzakhala m'dziko ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga, limene anakhalamo makolo anu, ndipo adzakhala m'mwemo iwo, ndi ana ao, ndi zidzukulu zao kosatha; ndi Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wao kosatha.

26Yes. 55.3; 2Ako. 6.16Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.

27Ezk. 36.28; Yoh. 1.14; Chiv. 21.3Kachisi wanganso adzakhala nao, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.

28Ezk. 36.23Ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakupatula Israele, pokhala pakati pao malo anga opatulika kosatha.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help