1Ana a Isakara ndiwo Tola, ndi Puwa, Yasubu ndi Simironi; anai.
2Ndi ana a Tola: Uzi, ndi Refaya, ndi Yeriyele, ndi Yamai, ndi Ibisamu, ndi Semuele, akulu a nyumba za makolo; ao ndiwo a Tola, ngwazi zamphamvu, m'mibadwo yao; kuwerenga kwao, masiku a Davide ndiko zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi limodzi.
3Ndi mwana wa Uzi: Izrahiya; ndi ana a Izrahiya: Mikaele, ndi Obadiya, ndi Yowele, ndi Isiya; onse asanuwa ndiwo akulu.
4Ndi pamodzi nao mwa mibadwo yao, mwa nyumba za makolo ao, panali magulu a nkhondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi, popeza anachuluka akazi ao ndi ana ao.
5Ndi abale ao mwa mabanja onse a Isakara, ngwazi zamphamvu, oyesedwa mwa chibadwidwe chao, onsewa ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu zisanu ndi ziwiri.
Adzukulu a Benjamini ndi Nafutali6Ana a Benjamini ndiwo Bela, ndi Bekere, ndi Yediyaele, atatu.
7Ndi ana a Bela: Eziboni, ndi Uzi, ndi Uziyele, ndi Yerimoti, ndi Iri, asanu; akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu, owerengedwa m'mabuku a chibadwidwe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza makumi atatu ndi anai.
8Ndi ana a Bekere: Zimira, ndi Yowasi, ndi Eliyezere, ndi Eliyoenai, ndi Omuri, ndi Yeremoti, ndi Abiya, ndi Anatoti, ndi Alemeti. Onsewa ndiwo ana a Bekere.
9Ndipo anayesedwa mwa chibadwidwe chao, mwa mibadwo yao, akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu zikwi makumi awiri mphambu mazana awiri.
10Ndi mwana wa Yediyaele: Bilihani; ndi ana a Bilihani: Yeusi, ndi Benjamini, ndi Ehudi, ndi Kenana, ndi Zetani, ndi Tarisisi, ndi Ahisahara.
11Onsewa ndiwo ana a Yediyaele; ndiwo akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu zikwi khumi mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana awiri akutuluka kugulu kunkhondo.
12Supimu yemwe ndi Hupimu ana a Iri, ndi Husimu mwana wa Aheri.
13Ana a Nafutali: Yaziyele, ndi Guni, ndi Yezere, ndi Salumu, ana a Biliha.
Adzukulu a Manase14Ana a Manase ndiwo Asiriele amene mkazi wake anambala. Koma mkazi wake wamng'ono Mwaramu anabala Makiri atate wa Giliyadi;
15Num. 27.1ndi Makiri anadzitengera mkazi, mlongo wake wa Hupimu ndi Supimu, dzina lake ndiye Maaka. Ndipo dzina la mwana wachiwiri wa Manase ndiye Zelofehadi. Ndi Zelofehadi anali ndi ana akazi.
16Ndi Maaka mkazi wa Makiri anabala mwana, namutcha dzina lake Peresi, ndi dzina la mbale wake ndiye Seresi, ndi ana ake ndiwo Ulamu, ndi Rakemu.
17Ndi mwana wa Ulamu: Bedani; ndiwo ana a Giliyadi mwana wa Makiri mwana wa Manase.
18Ndi mlongo wake Hamoleketi anabala Isihodi, ndi Abiyezere, ndi Mala.
19Ndi ana a Semida ndiwo Ahiyani, ndi Sekemu, ndi Liki, ndi Aniyamu.
A Efuremu20 Num. 26.35 Ndi ana a Efuremu: Sutela, ndi Beredi mwana wake, ndi Tahati mwana wake, ndi Eleada mwana wake, ndi Tahati mwana wake,
21ndi Zabadi mwana wake, ndi Sutela mwana wake, ndi Ezere, ndi Eleadi, amene anthu a Gati obadwa m'dziko anamupha, popeza anatsikira kukalanda zoweta zao.
22Ndipo Efuremu atate wao, anachita maliro masiku ambiri, ndi abale ake anadza kudzamtonthoza mtima.
23Ndipo analowa kwa mkazi wake, naima iye, nabala mwana, namutcha dzina lake Beriya, popeza m'nyumba mwake mudaipa.
24Ndipo mwana wake wamkazi ndiye Seera, amene anamanga Betehoroni wa kunsi, ndi Betehoroni wa kumtunda, ndi Uzeniseera.
25Ndipo Refa anali mwana wake, ndi Resefi, ndi Tela mwana wake, ndi Tahani mwana wake,
26Ladani mwana wake, Amihudi mwana wake, Elisama mwana wake,
27Nuni mwana wake, Yoswa mwana wake.
28Ndipo dziko lao, ndi pokhala pao ndizo Betele ndi milaga yake, ndi kum'mawa Naarani, ndi kumadzulo Gezere ndi milaga yake, ndi Sekemu ndi milaga yake, mpaka Aya ndi milaga yake;
29ndi kumalire a ana a Manase; Beteseani ndi milaga yake, Taanaki ndi milaga yake, Megido ndi milaga yake, Dori ndi milaga yake. M'menemo anakhala ana a Yosefe mwana wa Israele.
30Ana a Asere: Imina, ndi Isiva, ndi Isivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao.
31Ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikiele, ndiye atate wa Birizaiti.
32Ndi Hebere anabala Yafileti, ndi Somere, ndi Hotamu, ndi Suwa mlongo wao.
33Ndi ana a Yafileti: Pasaki, ndi Bimala, ndi Asivati. Awa ndi ana a Yafileti.
34Ndi ana a Semeri: Ahi, ndi Roga, Yehuba, ndi Aramu.
35Ndi ana a Helemu mbale wake: Zofa, ndi Imina, ndi Selesi, ndi Amala.
36Ana a Zofa: Suwa, ndi Harenefere, ndi Suwala, ndi Beri, ndi Imira,
37Bezere, ndi Hodi, ndi Sama, ndi Silisa, ndi Itirani, ndi Beera.
38Ndi ana a Yetere: Yefune, ndi Pisipa, ndi Ara.
39Ndi ana a Ula: Ara, ndi Haniyele, ndi Riziya.
40Awa onse ndiwo ana a Asere, akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zosankhika ndi zamphamvu, akulu mwa akalonga. Oyesedwa mwa chibadwidwe chao otumikira kunkhondo ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.