1Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Ndiloleni ndisankhe tsopano anthu zikwi khumi ndi ziwiri, ndipo ndidzanyamuka usiku womwe uno ndi kulondola Davide;
2Davide ndi anthu ake aoloka Yordani
21Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anatuluka m'chitsime, namka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofele anapangira zotere pa inu.
22Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordani. Kutacha m'mawa sanasowe mmodzi wa iwo wosaoloka Yordani.
232Maf. 20.1; Mat. 27.5Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumudzi kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.
Abisalomu ndi anthu ake aolokanso Yordani24 Gen. 32.2 Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordani, iye ndi anthu onse a Israele pamodzi naye.
25Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.
26Ndipo Israele ndi Abisalomu anamanga zithando m'dziko la Giliyadi.
Nkhondo imlaka Abisalomu, naphedwa iye mwini27 2Sam. 19.13-32 Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,
28iwo anabwera nao makama, ndi mbale, ndi zotengera zadothi, ndi tirigu, ndi barele, ndi ufa, ndi tirigu wokazinga, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi zokazinga zina,
29ndi uchi ndi mafuta, ndi nkhosa, ndi mase a ng'ombe, kuti adye Davide, ndi anthu amene anali naye; pakuti anati, Anthu ali ndi njala, olema, ndi aludzu m'chipululumo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.