3 YOHANE 1 - Buku Lopatulika Bible 2014

1 2Yoh. 1 Mkuluyo kwa Gayo wokondedwayo, amene ndikondana naye m'choonadi.

2Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera.

32Yoh. 4Pakuti ndinakondwera kwakukulu, pofika abale ndi kuchita umboni za choonadi chako, monga umayenda m'choonadi.

Za kuchereza abale ndi alendo

4 1Ako. 4.15 Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m'choonadi.

5Wokondedwa, uchita chokhulupirika nacho chilichonse, uwachitira abale ndi alendo omwe;

6amene anachita umboni za chikondi chako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzachita bwino:

71Ako. 9.12, 15pakuti chifukwa cha dzinali anatuluka, osalandira kanthu kwa amitundu.

8Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana nacho choonadi.

Za Diotrefe ndi Demetrio

9Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife.

10Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, zakunena zopanda pake pa ife ndi mau oipa; ndipo popeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mu Mpingo.

11Yes. 1.16-17; 1Yoh. 2.29Wokondedwa, usatsanza chili choipa komatu chimene chili chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu; iye wakuchita choipa sanamuona Mulungu.

12Yoh. 21.24; 1Tim. 3.7Demetrio, adamchitira umboni anthu onse, ndi choonadi chomwe; ndipo ifenso tichita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona.

13Ndinali nazo zambiri za kukulembera, komatu sindifuna kukulembera ndi kapezi ndi peni;

14koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana.

15Mtendere ukhale nawe. Akupereka moni abwenzi. Upereke moni kwa abwenzi ndi kutchula maina ao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help