1Wakhazikika mtima wanga, Mulungu;
ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga.
2Galamukani, chisakasa ndi zeze;
ndidzauka ndekha mamawa.
3Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova:
ndipo ndidzaimba zakukulemekezani mwa anthu.
4Pakuti chifundo chanu nchachikulu kupitirira kumwamba,
ndi choonadi chanu kufikira mitambo.
5Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu;
ndi ulemerero wanu pamwamba pa dziko lonse lapansi,
6kuti okondedwa anu alanditsidwe,
pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutivomereze.
7Mulungu analankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera:
ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.
8Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga;
ndi Efuremu ndiye mphamvu ya mutu wanga;
Yuda ndiye wolamulira wanga.
9Mowabu ndiye mkhate wanga;
pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga;
ndidzafuulira Filistiya.
10Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga?
Adzanditsogolera ndani ku Edomu?
11Si ndinu Mulungu, amene mwatitaya
osatuluka nao magulu athu?
12Tithandizeni mumsauko;
pakuti chipulumutso cha munthu ndi chabe.
13Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima:
Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.