2 SAMUELE Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014

Mau OyambaBukuli likukamba za ufumu wa Davide ndiponso za nkhondo zimene iye anamenya ndi adani ake m'dziko mwake ndiponso ndi maiko oyandikana ndi dziko la Israele, pofuna kulimbitsa ndi kukulitsa ufumu wakewo.Davide anali munthu wa chikhulupiriro cholimba ndi wokonda Mulungu kwambiri, ndipo amadziwa kukopa mitima ya anthu ake. Komabe nthawi zina anagwa m'machimo oopsa chifukwa chotsata zilakolako ndi zikhumbitso zoipa. Mneneri Natani atamdzudzula chifukwa cha zoipazo, iye anadzichepetsa navomera kuti walakwadi nkuvomera chilango chimene Mulungu apereka.Aisraele adatengeka mtima ndi mfumu Davide, ndipo patapita zaka zambiri, pamene dziko lao lidapasuka, Aisraelewo ankakumbukira khalidwe lake abwino ndi ntchito zake zazikulu, kotero kuti ankalakalaka kukhalanso ndi mfumu ina yokhala ndi mtima ngati wa Davide, pakati pa zidzukulu zake.Za mkatimuUfumu wa Davide mu dziko la Yuda 1.1—4.12

Ufumu wa Davide m'dziko lonse la Israele 5.1—24.25

a. Zaka zoyamba 5.1—10.19

b. Davide ndi Bateseba 11.1—12.25

c. Ana ake amuukira ndiponso zovuta zina 12.26—20.26

d. Zaka zotsiriza za ufumu wake 21.1—24.25

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help