1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu chifukwa cha wakufa mwa anthu a mtundu wake;
2koma chifukwa cha abale ake enieni ndiwo, mai wake, ndi atate wake, ndi mwana wake wamwamuna, ndi mwana wake wamkazi, ndi mbale wake;
3ndi chifukwa cha mlongo wake weniweni, akakhala namwali wosakhala naye mwamuna, nkuloleka adzidetse chifukwa cha iwowa.
4Akakhala mwini banja pakati pa anthu a mtundu wake, asadzidetse, ndi kudziipsa.
5Asamete tsitsi la pamtu pao, kapena kuchecherera ndevu zao, kapena kudzicheka matupi ao.
6Lev. 20.26Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; chifukwa chake akhale opatulika.
7Asadzitengere mkazi wachigololo, kapena woipsidwa; asatenge mkazi woti adamchotsa mwamuna wake; popeza apatulikira Mulungu wake.
8Lev. 20.7Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera,
9Akadziipsa mwana wamkazi wa wansembe ndi kuchita chigololo, alikuipsa atate wake, amtenthe ndi moto.
10Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ake, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pake, amene anamdzaza dzanja kuti avale zovalazo, asawinde, kapena kung'amba zovala zake.
11Asafike kuli mtembo; asadzidetse chifukwa cha atate wake, kapena mai wake.
12Asatuluke m'malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wake; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wake ali pa iye; Ine ndine Yehova.
13Ndipo adzitengere mkazi akali namwali.
14Mkazi wamasiye, kapena womleka, kapena woipsidwa, wachigololo, oterewa asawatenge; koma azitenga namwali wa anthu a mtundu wake akhale mkazi wake.
15Asaipse mbeu yake mwa anthu a mtundu wake; popeza Ine ndine Yehova wakumpatula iye.
Ansembe akhale opanda chilema pathupi16Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
17Lev. 22.21Nena ndi Aroni, kuti, Aliyense wa mbeu zako mwa mibadwo yao wakukhala nacho chilema, asayandikize kupereka mkate wa Mulungu wake.
18Pakuti munthu aliyense wokhala nacho chilema, asayandikize; wakhungu, kapena wotsimphina, kapena wopunduka mphuno, kapena wamkulu chiwalo,
19kapena munthu wopunduka phazi kapena wopunduka dzanja,
20kapena wowerama, kapena wamfupi msinkhu, kapena wopunduka diso, kapena munthu wamphere, kapena wachipere, kapena wopunduka kumoto.
21Wa mbeu ya Aroni wansembe asayandikize mmodzi wokhala nacho chilema, kupereka nsembe zamoto za Yehova; ali nacho chilema asayandikize kupereka chakudya cha Mulungu wake.
22Adye chakudya cha Mulungu wake, chopatulika kwambiri, ndi chopatulika;
23koma asafike ku nsalu yotchinga, asayandikize ku guwa la nsembe, popeza ali nacho chilema; kuti angaipse malo anga opatulika; popeza Ine ndine Yehova wakuwapatula.
24Momwemo Mose ananena ndi Aroni, ndi ana ake amuna, ndi ana onse a Israele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.