1 Yes. 40.11; Yer. 23.3-4; Ezk. 34.11-12, 23; Yoh. 10.11; Afi. 4.19 Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.
2 Ezk. 34.14; Chiv. 7.17 Andigonetsa kubusa lamsipu,
anditsogolera kumadzi odikha.
3Atsitsimutsa moyo wanga;
anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.
4 Yob. 10.21-22; Mas. 27.1; Yes. 43.2 Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa,
sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine;
chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
5 Mas. 45.7; 92.10 Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga;
mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.
6Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata
masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.