1 Mas. 71.1-3 Ndakhulupirira Inu, Yehova,
ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse,
mwa chilungamo chanu ndipulumutseni ine.
2Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga.
Mundikhalire ine thanthwe lolimba,
nyumba yamalinga yakundisunga.
3Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa;
ndipo chifukwa cha dzina lanu
ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.
4Mundionjole m'ukonde umene ananditchera mobisika.
Pakuti Inu ndinu mphamvu yanga.
5 Luk. 23.46; Mac. 7.59 Ndipereka mzimu wanga m'dzanja lanu;
mwandiombola, Inu Yehova, Mulungu wa choonadi.
6 Yon. 2.8 Ndikwiya nao iwo akusamala zachabe zonama,
koma ndikhulupirira Yehova.
7Ndidzakondwera ndi kusangalala m'chifundo chanu,
pakuti mudapenya zunzo langa;
ndipo mudadziwa mzimu wanga mu nsautso yanga.
8Ndipo simunandipereka m'dzanja la mdani;
munapondetsa mapazi anga pali malo.
9 Mas. 6.2, 7, 10 Mundichitire chifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine.
Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga,
zapuwala ndi mavuto.
10Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni,
ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo.
Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga,
ndi mafupa anga apuwala.
11Ndakhala chotonza chifukwa cha akundisautsa onse,
inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa choopsa;
iwo akundipenya pabwalo anandithawa.
12Ndaiwalika m'mtima monga wakufa,
ndikhala monga chotengera chosweka.
13 Mat. 27.1 Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri,
mantha andizinga.
Pondipangira chiwembu,
anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.
14Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova,
ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga.
15 Yob. 14.5; 24.1 Nyengo zanga zili m'manja mwanu,
mundilanditse m'manja a adani anga,
ndi kwa iwo akundilondola ine.
16 Num. 6.25-26 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu,
mundipulumutse ndi chifundo chanu.
17 Mas. 31.1 Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu,
oipa achite manyazi, atonthole m'manda.
18 Mas. 101.7 Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza,
imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima,
ndi kudzikuza ndi kunyoza.
19 Yes. 64.4; 1Ako. 2.9 Ha! Kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga,
kumene munasungira iwo akuopa Inu,
kumene munachitira iwo akukhulupirira Inu,
pamaso pa ana a anthu!
20 Mas. 32.7; Yob. 5.21 Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu,
mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse
pa kutetana kwa malilime.
21Wolemekezeka Yehova,
pakuti anandichitira chifundo chake chodabwitsa
m'mudzi walinga.
22Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati,
Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu.
Komatu munamva mau a kupemba kwanga
pamene ndinafuulira kwa Inu.
23Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake,
Yehova asunga okhulupirika,
ndipo abwezera zochuluka iye wakuchita zodzitama.
24 Mas. 27.1 Limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu,
inu nonse akuyembekeza Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.