1Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,
2Yer. 23.1; Zek. 11.17; Yoh. 10.11Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?
3Yes. 56.11Mukudya mafuta, muvala ubweya, mukupha zonenepa; koma simudyetsa nkhosa.
4Zek. 11.16; Luk. 15.4Zofooka simunazilimbitsa; yodwala simunaichiritsa, yothyoka simunailukira chika, yopirikitsidwa simunaibweza, yotayika simunaifuna; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa.
51Maf. 22.17; Mat. 9.36M'mwemo zinamwazika posowa mbusa, nizinakhala chakudya cha zilombo zilizonse za kuthengo, popeza zinamwazika.
6Nkhosa zanga zinasokera kumapiri ali onse, ndi pa chitunda chilichonse chachitali; inde nkhosa zanga zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna.
7Chifukwa chake abusa inu, imvani mau a Yehova:
81Maf. 22.17; Yer. 23.1; Zek. 11.17; Mat. 9.36Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala chakudya cha zilombo zonse za kuthengo, chifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunafune nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;
9chifukwa chake, abusa inu, imvani mau a Yehova:
10Aheb. 13.17Atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine ndiipidwa nao abusa, ndidzafunsa nkhosa zanga pa dzanja lao, ndi kuwaletsa asadyetsenso nkhosazo, ngakhale kudzidyetsa okha sadzachitanso; ndipo ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pao, zisakhale chakudya chao.
11Luk. 19.10; Yoh. 10.11Pakuti atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna.
12Zek. 11.16; Luk. 15.4Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.
13Yes. 65.9-10Ndipo ndidzazitulutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m'maiko, ndi kulowa nazo m'dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israele, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m'dziko.
14Mas. 23.2; Yes. 40.11Ndidzazidyetsa podyetsa pabwino; ndi pa mapiri atali a Israele padzakhala kholo lao, apo adzagona m'khola mwabwino, nadzadya podyetsa pokometsera pa mapiri a Israele.
15Mas. 23.2; Yes. 40.11Ine ndekha ndidzadyetsa nkhosa zanga, ndi kuzigonetsa, ati Ambuye Yehova.
16Yes. 61.1; Yer. 10.24; Luk. 19.10Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.
17Mat. 25.32-33Ndipo inu, gulu langa, atero Ambuye Yehova, ndiweruza pakati pa zoweta ndi zoweta, nkhosa zamphongo ndi atonde.
18Kodi chikucheperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? Muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? Muyenera kumwa madzi odikha, ndi kuvundulira otsalawo ndi mapazi anu?
19Ndi nkhosa zanga zidye kodi zoponderezeka ndi mapazi anu, ndi kumwa zovunduliridwa ndi mapazi anu?
20 Mat. 25.32-33 Chifukwa chake atero nao Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzaweruza pakati pa zoweta zonenepa, ndi zoweta zoonda.
21Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo,
22Mat. 25.32-33chifukwa chake ndidzapulumutsa gulu langa lisakhalenso chakudya; ndipo ndidzaweruza pakati pa zoweta ndi zoweta.
23Yer. 23.4-5; Yoh. 10.11Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala mbusa wao.
24Eks. 29.45Ndipo Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wao, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pao; Ine Yehova ndanena.
25Yes. 54.10; Ezk. 37.26Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.
26Gen. 12.2; Zek. 8.13; Mala. 3.10Pakuti ndidzaika izi ndi milaga yozungulira chitunda changa, zikhale mdalitso; ndipo ndidzavumbitsa mivumbi m'nyengo yake, padzakhala mivumbi ya madalitso.
27Lev. 26.13Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.
28Ezk. 34.25Ndipo sadzakhalanso chakudya cha amitundu, ndi chilombo cha kuthengo sichidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.
29Yes. 11.1Ndipo ndidzawautsira mbeu yomveka, ndipo sadzachotsedwanso ndi njala m'dzikomo, kapena kusenzanso manyazi a amitundu.
30Ezk. 37.27Ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wao ndili nao, ndi kuti iwo, nyumba ya Israele, ndiwo anthu anga, ati Ambuye Yehova.
31Mas. 100.3Ndipo inu nkhosa zanga, nkhosa zapabusa panga, ndinu anthu, ndi Ine ndine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.