1 1Maf. 1.33-39 Atakalamba tsono Davide ndi kuchuluka masiku, iye analonga mwana wake Solomoni akhale mfumu ya Israele.
2Ndipo anasonkhanitsa akulu onse a Israele, ndi ansembe ndi Alevi.
3Num. 4.3, 47Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo chiwerengo chao kuwawerenga mmodzimmodzi ndicho amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu.
4A iwowa zikwi makumi awiri mphambu zinai anayang'anira ntchito ya nyumba ya Yehova, ndi zikwi zisanu ndi chimodzi ndiwo akapitao ndi oweruza,
5ndi zikwi zinai odikira; ndi zikwi zinai analemekeza Yehova ndi zoimbira zimene ndinazipanga, anati Davide, kuti alemekeze nazo.
6Num. 26.57Ndipo Davide anawagawa magawo monga mwa ana a Levi: Geresoni, Kohati, ndi Merari.
7A Ageresoni: Ladani ndi Simei.
8Ana a Ladani: wamkulu ndi Yehiyele, ndi Zetamu, ndi Yowele; atatu.
9Ana a Simei: Selomoti, ndi Haziyele, ndi Harani; atatu. Ndiwo akulu a nyumba za makolo a Ladani.
10Ndi ana a Simei: Yahati, Zina, ndi Yeusi, ndi Beriya. Awa anai ndiwo ana a Simei.
11Wamkulu wa iwo ndi Yahati, mnzake ndi Ziza; koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri, potero anakhala nyumba ya kholo yowerengedwa pamodzi.
12Ana a Kohati: Amuramu, Izihara, Hebroni, ndi Uziyele; anai.
13Eks. 28.1; Num. 6.23-26Ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulika kwambiri, iye ndi ana ake, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kosatha.
14Kunena za Mose munthu wa Mulunguyo, ana ake anatchulidwa mwa fuko la Levi.
15Ana a Mose: Geresomo, ndi Eliyezere.
16Ana a Geresomo: wamkulu ndi Sebuele.
17Ndi ana a Eliyezere: wamkulu ndi Rehabiya. Ndipo Eliyezere analibe ana ena, koma ana a Rehabiya anachuluka kwambiri.
18Ana a Izihara: wamkulu ndiye Selomiti.
19Ana a Hebroni: wamkulu ndi Yeriya, wachiwiri ndi Amariya, wachitatu ndi Yahaziele, wachinai ndi Yekameamu.
20Ana a Uziyele: wamkulu ndi Mika, wachiwiri ndi Isiya.
21Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi ana a Mali: Eleazara ndi Kisi.
22Nafa Eleazara wopanda ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndi asuweni ao ana a Kisi anawatenga akhale akazi ai.
23Ana a Musi: Mali, ndi Edere, ndi Yeremoti; atatu.
24Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa chiwerengero cha maina mmodzimmodzi, akugwira ntchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
251Mbi. 22.18Pakuti Davide anati, Yehova Mulungu wa Israele wapumulitsa anthu ake; ndipo akhala m'Yerusalemu kosatha;
26Num. 4.5-15ndiponso Alevi asasenzenso Kachisi ndi zipangizo zake zonse za utumiki wake.
27Pakuti monga mwa mau ake otsiriza a Davide, ana a Levi anawerengedwa kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
28Pakuti ntchito yao ndiyo kuimirira ana a Aroni, atumikire m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo, ndi kuzipinda, ndi kuyeretsa zopatulika zonse; inde ntchito za utumiki wa nyumba ya Mulungu;
29Lev. 6.20-23ya mkate woonekera womwe, ndi ya ufa wosalala wa nsembe yaufa, ndi ya timitanda taphanthiphanthi topanda chotupitsa, ndi ya chiwaya, ndi yakukazinga, ndi ya miyeso iliyonse;
30ndi kuimirira m'mawa ndi m'mawa kuyamika ndi kulemekeza Yehova, momwemonso madzulo;
31Num. 10.10ndi kupereka nsembe zopsereza zonse kwa Yehova, za masabata, za pokhala mwezi, za nyengo zoikika, kuwerenga kwake monga mwa lemba lake, kosalekeza pamaso pa Yehova;
32Num. 1.53; 3.6-9ndi kuti asunge udikiro wa chihema chokomanako, ndi udikiro wa malo opatulika ndi udikiro wa ana a Aroni abale ao, potumikira nyumba ya Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.