1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2Dzipangire malipenga awiri asiliva; uwasule mapangidwe ake; uchite nao poitana khamu, ndi poyendetsa a m'zigono.
3Yer. 4.5Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la chihema chokomanako.
4Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akulu a zikwi a m'Israele, azisonkhana kuli iwe.
5Mukaliza chokweza ayende a m'zigono za kum'mawa.
6Mukalizanso chokweza, a m'zigono za kumwera ayende; alize chokweza pakumuka.
7Pomemeza msonkhano mulize, wosati chokweza ai.
8Ana amuna a Aroni, ansembe, ndiwo aziliza malipenga; ndipo akhale kwa inu lemba losatha ku mibadwo yanu.
9Mas. 98.3; 106.4Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kuchita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize chokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukira inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.
10Mas. 81.3Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu chikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Aisraele achoka ku Sinai11Ndipo kunachitika, chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la makumi awiri la mweziwo, kuti mtambo unakwera kuchokera kwa Kachisi wa mboni.
12Ndipo ana a Israele anayenda monga mwa maulendo ao, kuchokera m'chipululu cha Sinai; ndi mtambo unakhala m'chipululu cha Parani.
13Potero anayamba ulendo wao monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.
14Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.
15Ndi pa gulu la fuko la ana a Isakara panali Netanele mwana wa Zuwara.
16Ndi gulu la fuko la ana a Zebuloni panali Eliyabu mwana wa Heloni.
17Ndipo anagwetsa Kachisi; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula Kachisi, anamuka naye.
18Ndi a mbendera ya chigono cha Rubeni, anayenda monga mwa magulu ao; ndipo pa gulu lake anayang'anira Elizuri mwana wa Sedeuri.
19Ndi pa gulu la fuko la ana a Simeoni anayang'anira Selumiele mwana wa Zurishadai.
20Ndi pa gulu la fuko la ana a Gadi anayang'anira Eliyasafu mwana wa Deuwele.
21Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu Kachisi asanafike iwowa.
22Ndipo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Efuremu, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Elisama mwana wa Amihudi.
23Ndi pa gulu la fuko la ana a Manase anayang'anira Gamaliele mwana wa Pedazuri.
24Ndi pa gulu la fuko la ana a Benjamini anayang'anira Abidani mwana wa Gideoni.
25Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.
26Ndi pa gulu la fuko la ana a Asere anayang'anira Pagiyele mwana wa Okarani.
27Ndi pa gulu la fuko la ana a Nafutali anayang'anira Ahira mwana wa Enani.
28Potero maulendo a ana a Israele anakhala monga mwa magulu ao; nayenda ulendo wao.
Mose apempha Hobabu awaperekeze29 Gen. 12.7; 32.12 Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reuwele Mmidiyani mpongozi wa Mose, Ife tili kuyenda kunka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakuchitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israele zokoma.
30Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga.
31Yob. 29.15Koma anati, Usatisiyetu; popeza udziwa poyenera kumanga ife m'chipululu, ndipo udzakhala maso athu.
32Ndipo kudzatero, ukamuka nafe, inde, kudzali kuti zokoma zilizonse Yehova atichitira ife, zomwezo tidzakuchitira iwe.
33 Mas. 132.8; Yer. 31.2 Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.
34Ndipo mtambo wa Yehova unali pamwamba pao msana, pakuyenda iwo kuchokera kuchigono.
35Mas. 68.1Ndipo kunali pakuchokera kunka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu.
36Ndi pakupumula ili anati, Bwerani Yehova kwa zikwizikwi za Israele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.