EKSODO 39 - Buku Lopatulika Bible 2014

Maombedwe a zovala za ansembe

1Ndipo anaomba zovala zakutumikira nazo ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, atumikire nazo m'malo opatulika, naomba zovala zopatulika za Aroni; monga Yehova adamuuza Mose.

2 Eks. 28.1-43 Ndipo anaomba efodi wa golide, lamadzi, lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

3Ndipo anasula golide waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri.

4Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pa nsonga ziwirizo anamlumikiza.

5Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa chiombedwe chomwechi; wa golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose.

6Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolide, yolocha ngati malochedwe a chosindikizira, ndi maina a ana a Israele.

7Ndipo anaiika pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso kwa ana a Israele; monga Yehova adamuuza Mose.

8Ndipo anaomba chapachifuwa, ntchito ya mmisiri, monga maombedwe ake a efodi; cha golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

9Chinakhala chaphwamphwa; anachiomba chapachifuwa chopindika; utali wake dzanja limodzi, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, chinakhala chopindika.

10Ndipo anaika pomwepo mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba.

11Ndi mzere wachiwiri wa nofeki, safiro, ndi yahalomu.

12Ndi mzere wachitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama.

13Ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; inakhala yogwirika ndi golide maikidwe ake.

14Ndipo miyalayi inakhala monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga mwa maina ao; ngati malochedwe a chosindikizira, yonse monga mwa maina ake, kwa mafuko khumi ndi awiriwo.

15Ndipo anapangira pachapachifuwa maunyolo ngati zingwe, ntchito yopota ya golide woona.

16Anapanganso zoikamo ziwiri zagolide, ndi mphete ziwiri zagolide; naika mphete ziwirizo pa nsonga ziwiri za chapachifuwa.

17Ndipo anamanga maunyolo awiri opota agolide pa mphete ziwiri pa nsonga za chapachifuwa.

18Ndi nsonga zake ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m'tsogolo mwake.

19Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pa nsonga ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake m'katimo, pa mbali ya kuefodi.

20Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pake, pa mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi.

21Ndipo anamanga chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose.

22Ndipo anaomba mwinjiro wa efodi, ntchito yoomba ya lamadzi lokha;

23ndi pakati pake polowa mutu, ngati polowa pa malaya ochingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pake, pangang'ambike.

24Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

25Ndipo anapanga miliu ya golide woona, napakiza miliu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza.

26Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose.

27Ndipo anaomba malaya a bafuta, a ntchito yoomba, a Aroni, ndi a ana ake amuna,

28ndi nduwira yabafuta wa thonje losansitsa, ndi akapa okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zovala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa,

29ndi mpango wabafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ntchito ya wopikula; monga Yehova adamuuza Mose.

30 Eks. 28.36 Ndipo anapanga phanthiphanthi wa korona wopatulika wa golide woona, nalembapo lemba, ngati malochedwe a chosindikizira, KUPATULIKIRA YEHOVA.

31Namangako mkuzi wamadzi, kuumanga nao pamwamba pa nduwira; monga Yehova adamuuza Mose.

32Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.

Zopangidwa zonse zionetsedwa kwa Mose

33Ndipo anabwera naye Kachisi kwa Mose, chihemacho, ndi zipangizo zake zonse, zokowera zake, matabwa ake, mitanda yake, ndi mizati yake, nsanamira zake ndi nsichi zake, ndi makamwa ake;

34ndi chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi nsalu yotchinga yotsekera;

35likasa la mboni, ndi mphiko zake, ndi chotetezerapo;

36gomelo, zipangizo zake zonse, ndi mkate woonekera;

37choikapo nyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira;

38ndi guwa la nsembe lagolide, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho;

39guwa la nsembe la mkuwa, ndi sefa wake wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake;

40nsalu zochingira za pabwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, zingwe zake, ndi zichiri zake, ndi zipangizo zonse za ntchito ya Kachisi, za ku chihema chokomanako;

41zovala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe.

42Monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, momwemo ana a Israele anachita ntchito zonse.

432Sam. 6.18; 2Mbi. 6.3Ndipo Mose anaona ntchito zonse, ndipo, taonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help