1 Yos. 22.22 Mulungu wa milungu, Yehova, wanena,
aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa
kufikira kulowa kwake.
2Mulungu awalira m'Ziyoni, mokongola mwangwiro.
3 Lev. 10.2; Mas. 97.3 Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete.
Moto udzanyeka pankhope pake,
ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu.
4Kumwamba adzaitana zakumwamba,
ndi dziko lapansi, kuti aweruze anthu ake.
5 Deut. 33.3; Yes. 13.3 Mundisonkhanitsire okondedwa anga;
amene anapangana ndi Ine ndi nsembe.
6 Mas. 97.6 Ndipo zakumwamba zionetsera chilungamo chake;
pakuti Mulungu mwini wake ndiye woweruza.
7 Mas. 81.8 Imvani, anthu anga, ndipo ndidzanena;
Israele, ndipo ndidzachita mboni pa iwe,
Ine Mulungu, ndine Mulungu wako.
8 Yes. 1.11; Yer. 7.22 Sindikudzudzula iwe chifukwa cha nsembe zako;
popeza nsembe zako zopsereza zili pamaso panga chikhalire.
9 Mik. 6.6; Mac. 17.25 Sindidzatenga ng'ombe m'nyumba mwako,
kapena mbuzi m'makola mwako.
10Pakuti zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga,
ndi ng'ombe za pa mapiri zikwi.
11Ndidziwa mbalame zonse za m'mapiri,
ndipo nyama za kuthengo zili ndi Ine.
12 Eks. 19.5; 1Ako. 10.26 Ndikamva njala, sindidzakuuza,
pakuti dziko lonse ndi langa, ndi kudzala kwake komwe.
13Kodi ndidzadya nyama ya ng'ombe,
kapena kumwa mwazi wa mbuzi?
14 Deut. 23.21; Aheb. 13.15 Pereka kwa Mulungu nsembe yachiyamiko;
numchitire Wam'mwambamwamba chowinda chako.
15 Mas. 91.15; 50.23 Ndipo undiitane tsiku la chisautso,
ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.
16Koma kwa woipa Mulungu anena,
Uli nao chiyani malemba anga kulalikira,
ndi kutchula pangano langa pakamwa pako?
17 Aro. 2.22-23 Popeza udana nacho chilangizo,
nufulatira mau anga.
18 Aro. 1.32 Pakuona mbala, uvomerezana nayo,
nuchita nao achigololo.
19 Mas. 52.2 Pakamwa pako mpochita zochimwa,
ndipo lilime lako likonza chinyengo.
20Ukhala, nuneneza mbale wako;
usinjirira mwana wa mai wako.
21 Mas. 90.8; Aro. 2.4 Izi unazichita iwe, ndipo ndinakhala chete Ine;
unayesa kuti ndifanana nawe,
ndidzakudzudzula, ndi kuchilongosola pamaso pako.
22 Yes. 51.13 Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu,
kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.
23 Mas. 27.6; Afi. 1.27 Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine;
ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake
ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.