1 2Pet. 1.13-14 Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, m'Mwamba.
2Aro. 8.26Pakutinso m'menemo tibuula, ndi kukhumbitsa kuvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera Kumwamba;
3ngatitu povekedwa sitidzapezedwa amaliseche.
41Ako. 15.53-54Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.
5Aef. 2.10Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife chikole cha Mzimu.
6Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tili kwathu m'thupi, sitili kwa Ambuye.
7Yoh. 20.29; Aro. 8.24-25(Pakuti tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe);
8Afi. 1.23koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m'thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye.
9Chifukwa chakenso tifunitsitsa, kapena kwathu kapena kwina, kukhala akumkondweretsa Iye.
10Mat. 25.31-32; Akol. 3.24-25Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.
Utumiki wa chiyanjanitso11 2Ako. 4.2; Aheb. 10.31 Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m'zikumbu mtima zanu.
12Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.
132Ako. 12.6, 11Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu.
14Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;
15Aro. 14.7-8ndipo adafera onse kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma mwa Iye amene adawafera iwo, nauka.
16Agal. 5.6; Akol. 3.11Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.
17Yoh. 3.3; Aro. 6.4; Aef. 2.15Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.
18Aro. 5.10Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso;
19Aro. 3.24-25ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a chiyanjanitso.
20 Aef. 6.20 Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
21Yes. 53.6, 9, 12; Agal. 3.13Ameneyo sanadziwa uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.