NUMERI 12 - Buku Lopatulika Bible 2014

Miriyamu ndi Aroni aukira Mose

1Ndipo Miriyamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose chifukwa cha mkazi mtundu wake Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi.

22Maf. 19.4; Yes. 37.4Ndipo anati, Kodi Yehova wanena ndi Mose yekha? Sananenanso ndi ife nanga? Ndipo Yehova anamva.

3Koma munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.

4Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriyamu modzidzimutsa, Tulukani inu atatu kudza ku chihema chokomanako. Pamenepo anatuluka atatuwo.

5Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la chihema, naitana Aroni ndi Miriyamu; natuluka onse awiri.

6Gen. 46.2; 1Maf. 3.5; Mat. 1.20; Luk. 1.11; Mac. 10.11Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.

7Aheb. 3.2, 5Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m'nyumba mwanga monse.

81Ako. 13.12; 2Pet. 2.10Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, moonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.

9Pamenepo Yehova anawapsera mtima iwo; nawachokera Iye.

102Maf. 5.27Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate.

112Sam. 24.10Ndipo Aroni anati kwa Mose, Mfumu yanga, musatiikiretu kuchimwa kumene tapusa nako, ndi kuchimwa nako.

12Asakhaletu iye ngati wakufa, amene dera lina la mnofu wake watha potuluka iye m'mimba mwa make.

13Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Mchiritsenitu, Mulungu.

14Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wake akadamlavulira malovu pankhope pake sakadachita manyazi masiku asanu ndi awiri? Ambindikiritse kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.

15Pamenepo anambindikiritsa Miriyamu kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo anthu sanayende ulendo kufikira atamlandiranso Miriyamu.

16Ndipo atatero anthuwo ananka ulendo wao kuchokera ku Hazeroti, namanga mahema ao m'chipululu cha Parani.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help