LEVITIKO 16 - Buku Lopatulika Bible 2014

Za tsiku lotetezera chaka ndi chaka

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, atamwalira ana amuna awiri a Aroni, muja anasendera pamaso pa Yehova, namwalira;

2Eks. 30.10; Aheb. 9.7ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.

3Aroni azilowa pa bwalo la malo opatulika nazozo: ng'ombe yamphongo ikhale ya nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale ya nsembe yopsereza.

4Avale malaya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zovala za kumiyendo pathupi pake, nadzimangire m'chuuno ndi mpango wabafuta, navale nduwira yabafuta; izi ndi zovala zopatulika; potero asambe thupi lake ndi madzi, ndi kuvala izi.

5Ndipo ku khamu la ana a Israele atenge atonde awiri akhale a nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo imodzi ikhale ya nsembe yopsereza.

6Aheb. 7.27-28Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nachite chodzitetezera iye yekha, ndi mbumba yake.

7Ndipo atenge mbuzi ziwirizo naziimike pamaso pa Yehova pakhomo pa chihema chokomanako.

8Ndipo Aroni ayese maere pa mbuzi ziwirizo; maere amodzi kwa Yehova, ndi amodzi kwa Azazele.

9Ndipo Aroni abwere nayo mbuzi imene adaigwera maere a Yehova, naiyese nsembe yauchimo.

10Koma mbuzi imene adaigwera maere a Azazele, aiike yamoyo pamaso pa Yehova, kuti achite nayo chotetezera, kuitumiza kuchipululu ikhale ya Azazele.

11Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nadzitetezere iye yekha, ndi mbumba yake, ndi kupha ng'ombe ya nsembe yauchimo ndiyo yakeyake;

12natenge mbale ya zofukiza yodzala ndi makala amoto, kuwachotsa pa guwa la nsembe, pamaso pa Yehova, ndi manja ake odzala ndi chofukiza chopera cha fungo lokoma, nalowe nayo m'tseri mwa nsalu yotchinga;

13naike chofukizacho pamoto pamaso pa Yehova, kuti mtambo wa chofukiza chiphimbe chotetezerapo chokhala pamboni, kuti angafe.

14Ndipo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi kuuwaza ndi chala chake pachotetezerapo, mbali ya kum'mawa; nawaze mwazi ndi chala chake chakuno cha chotetezerapo kasanu ndi kawiri.

15Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yauchimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wake m'tseri mwa nsalu yotchinga, nachite nao mwazi wake monga umo anachitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pachotetezerapo ndi chakuno cha chotetezerapo;

16Aheb. 9.22-23nachitire chotetezera malo opatulika, chifukwa cha kudetsedwa kwa ana a Israele, ndi chifukwa cha zolakwa zao, monga mwa zochimwa zao zonse; nachitire chihema chokomanako momwemo, chakukhala nao pakati pa zodetsa zao.

17Luk. 1.10, 21Ndipo musakhale munthu m'chihema chokomanako pakulowa iye kuchita chotetezera m'malo opatulika, kufikira atuluka, atachita chotetezera yekha, ndi mbumba yake, ndi msonkhano wonse wa Israele.

18Ndipo atulukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulichitira chotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.

19Ndipo awazepo mwazi wina ndi chala chake kasanu ndi katatu; ndi kuliyeretsa ndi kulipatula kulichotsera zodetsa za ana a Israele.

20Ndipo atatha kuchitira chotetezera malo opatulika, ndi chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, abwere nayo mbuzi yamoyo;

21Yes. 53.6; 2Ako. 5.21ndipo Aroni aike manja ake onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kuvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israele, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zochimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kuchipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu,

22Yes. 53.11; Aheb. 9.28ndi mbuziyo isenze yokha mphulupulu zonsezo kunka nazo ku dziko la pa lokha; ndipo azitaya mbuziyo m'chipululu.

23Pamenepo Aroni alowe m'chihema chokomanako, navule zovala zabafuta zimene anazivala polowa m'malo opatulika, nazisiye komweko.

24Ndipo asambe thupi lake ndi madzi kumalo kopatulika, navale zovala zake, natuluke, napereke nsembe yopsereza yake, ndi nsembe yopsereza ya anthu, nachite chodzitetezera yekha ndi anthu.

25Ndipo atenthe mafuta a nsembe yauchimo pa guwa la nsembe.

26Ndipo iye amene anachotsa mbuzi ipite kwa Azazele atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, ndipo atatero alowenso kuchigono.

27Lev. 16.16; Aheb. 13.11-12Koma ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndi mbuzi ya nsembe yauchimo, zimene mwazi wao analowa nao kuchita nao chotetezera m'malo opatulika, atuluke nazo kunja kwa chigono; natenthe ndi moto zikopa zao, ndi nyama zao, ndi chipwidza chao.

28Ndi iye amene anazitentha atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, ndipo atatero alowenso kuchigono.

29Ndipo lizikhala kwa inu lemba losatha; mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzichepetsa, osagwira ntchito konse, kapena wa m'dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu;

30popeza tsikuli adzachitira inu chotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukuchotserani zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova.

31Likhale kwa inu Sabata lakupumula, kuti mudzichepetse; ndilo lemba losatha.

32Ndipo wansembe, amene anamdzoza ndi kumdzaza dzanja lake achite ntchito ya nsembe m'malo mwa atate wake, achite chotetezera, atavala zovala zabafuta, zovala zopatulikazo.

33Ndipo achite chotetezera malo opatulikatu, natetezere chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; momwemo atetezerenso ansembe, ndi anthu onse a msonkhanowo.

34Ndipo ichi chikhale kwa inu lemba losatha, kuchita chotetezera ana a Israele, chifukwa cha zochimwa zao zonse, kamodzi chaka chimodzi. Ndipo anachita monga Yehova adauza Mose.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help