MASALIMO 99 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mulungu wamkulu wachifundo alemekezedwe

1

ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.

3 Deut. 28.58 Alemekeze dzina lanu lalikulu ndi loopsa.

Ili ndilo loyera.

4 Yes. 61.8 Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo;

Inu mukhazikitsa zolunjika,

muchita chiweruzo ndi chilungamo m'Yakobo.

5 1Mbi. 28.2 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,

ndipo gwadirani poponderapo mapazi ake:

Iye ndiye Woyera.

6 Eks. 14.15; 1Sam. 7.9 Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni,

ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake;

anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.

7 Eks. 33.9 Iye analankhula nao mu mtambo woti njo:

Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa.

8 Num. 14.20 Munawayankha, Yehova Mulungu wathu:

munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira,

mungakhale munabwezera chilango pa zochita zao.

9 Yes. 6.3 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,

ndipo gwadirani pa phiri lake loyera;

pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help