2 MBIRI 17 - Buku Lopatulika Bible 2014

Ukoma ndi ukulu wa Yehosafati

1 1Maf. 15.24 Ndipo Yehosafati mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake, nadzilimbitsa kuyambana ndi Israele.

2Naika ankhondo m'midzi yonse yamalinga ya Yuda, naika aboma m'dziko la Yuda, ndi m'midzi ya Efuremu, imene adailanda Asa atate wake.

3Ndipo Yehova anali ndi Yehosafati, popeza anayenda m'njira zake zoyamba za kholo lake Davide, osafuna Abaala;

4koma anafuna Mulungu wa kholo lake nayenda m'malamulo ake, osatsata machitidwe a Israele.

5Chifukwa chake Yehova anakhazikitsa ufumuwo m'dzanja lake, ndi onse Ayuda anabwera nayo mitulo kwa Yehosafati; ndipo zidamchulukira chuma ndi ulemu.

6Ndi mtima wake unakwezeka m'njira za Yehova; anachotsanso misanje ndi zifanizo m'Yuda.

7Chaka chachitatu cha ufumu wake anatuma akalonga ake, ndiwo Benihayili, ndi Obadiya, ndi Zekariya, ndi Netanele, ndi Mikaya, aphunzitse m'midzi ya Yuda;

8ndi pamodzi nao Alevi, ndiwo Semaya, ndi Netaniya, ndi Zebadiya, ndi Asahele, ndi Semiramoti, ndi Yehonatani, ndi Adoniya, ndi Tobiya, ndi Tobadoniya, Alevi; ndi pamodzi nao Elisama ndi Yehoramu, ansembe.

9Neh. 8.7Ndipo anaphunzitsa m'Yuda ali nalo buku la chilamulo la Yehova, nayendayenda m'midzi yonse ya Yuda, naphunzitsa mwa anthu.

102Mbi. 20.29Ndipo kuopsa kwa Yehova kunagwera maufumu a maiko ozungulira Yuda; momwemo sanayambane ndi Yehosafati.

11Ndipo Afilisti ena anabwera nazo kwa Yehosafati mitulo, ndi ndalama za msonkho; Aarabu omwe anabwera nazo kwa iye zoweta, nkhosa zamphongo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri ndi atonde zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri.

12Ndipo Yehosafati anakula chikulire, namanga m'Yuda nyumba zansanja, ndi midzi ya chuma.

13Nakhala nazo ntchito zambiri m'midzi ya Yuda, ndi anthu a nkhondo, ngwazi zamphamvu m'Yerusalemu.

14Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akulu a zikwi; Adina wamkulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu;

15ndi wotsatana naye mkulu Yehohanani, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu;

16Neh. 11.2ndi wotsatana naye Amasiya mwana wa Zikiri, wodzipereka kwa Yehova mwaufulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana awiri;

17ndi a Benjamini: Eliyada ngwazi yamphamvu, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri ogwira mauta ndi zikopa;

18wotsatana naye Yehozabadi, ndi pamodzi ndi iye okonzekeratu kunkhondo zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu.

192Mbi. 17.2Ndiwo amene analindirira mfumu, osawerenga iwo aja mfumu adawaika m'midzi yamalinga m'Yuda monse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help