1 Mac. 11.29; Aro. 15.26 Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu;
22Ako. 8.19, 24pakuti ndidziwa chivomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amasedoniya, kuti Akaya anakonzekeratu chitapita chaka; ndi changu chanu chinautsa ochulukawo.
32Ako. 8.6, 17-18, 22Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pake m'menemo; kuti, monga ndinanena, mukakhale okonzekeratu;
4kuti kapena akandiperekeze a ku Masedoniya nadzakupezani inu osakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingachititsidwe manyazi m'kulimbika kumene.
5Chifukwa chake ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti chikhale chokonzeka chomwechi, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.
6 Miy. 11.24; 19.1; 22.9 Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.
7Eks. 25.2; Mas. 41.1Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.
8Afi. 4.19Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;
9Mas. 112.9monga kwalembedwa,
Anabalalitsa, anapatsa kwa osauka;
chilungamo chake chikhale kunthawi yonse.
10 Yes. 55.9-10 Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu;
112Ako. 4.15polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.
12Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;
13Mat. 5.16popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino wa Khristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;
14ndipo iwo, ndi pempherero lao la kwa inu, akhumbitsa inu, chifukwa cha chisomo choposa cha Mulungu pa inu.
15Yak. 1.17Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.