1 Yer. 12.3 Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa.
2 2Maf. 19.27; Mat. 9.4; Yoh. 2.24-25 Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga,
muzindikira lingaliro langa muli kutali.
3Muyesa popita ine ndi pogona ine,
ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo.
4 Aheb. 4.13 Pakuti asanafike mau pa lilime langa,
taonani, Yehova, muwadziwa onse.
5Munandizinga kumbuyo ndi kumaso,
nimunaika dzanja lanu pa ine.
6Kudziwa ichi kundilaka ndi kundidabwitsa:
Kundikhalira patali, sindifikirako.
7 Yer. 23.24; Yon. 1.3 Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu?
Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?
8 Amo. 9.2-4 Ndikakwera kunka kumwamba, muli komweko;
kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko.
9Ndikadzitengera mapiko a mbandakucha,
ndi kukhala ku malekezero a nyanja;
10kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera,
nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.
11Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe,
ndi kuunika kondizinga kukhale usiku.
12 Dan. 2.22 Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu,
koma usiku uwala ngati usana;
mdima ukunga kuunika.
13Pakuti Inu munalenga impso zanga;
munandiumba ndisanabadwe ine.
14Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa
nchoopsa ndi chodabwitsa;
ntchito zanu nzodabwitsa;
moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.
15Thupi langa silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika,
poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi.
16Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya,
ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu,
masiku akuti ziumbidwe,
pakalibe chimodzi cha izo.
17 Mas. 40.5 Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu!
Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri!
18Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga:
Ndikauka ndikhalanso nanu.
19Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu:
Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine.
20 Yud. 15 Popeza anena za Inu moipa,
ndi adani anu atchula dzina lanu mwachabe.
21 2Mbi. 19.2 Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova?
Ndipo kodi sindimva nao chisoni iwo akuukira Inu?
22Ndidana nao ndi udani weniweni,
ndiwayesa adani.
23 Mas. 26.2 Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga;
mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.
24 Mas. 5.8 Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa,
nimunditsogolere pa njira yosatha.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.