1Tsegula pa makomo ako Lebanoni, kuti moto uthe mikungudza yako.
2Chema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; chemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yotchinjirizika yagwa pansi.
3Mau a kuchema kwa abusa! Pakuti ulemerero wao waipsidwa; mau a kubangula kwa misona ya mikango! Pakuti kudzikuza kwa Yordani kwaipsidwa.
4Zek. 11.7Atero Yehova Mulungu wanga: Dyetsani zoweta zakukaphedwa;
5zimene eni ake azipha, nadziyesera osapalamula; ndi iwo akuwagulitsa akuti, Alemekezedwe Yehova, pakuti ine ndine wolemera; ndi abusa ao sazichitira chifundo.
6Pakuti sindidzachitiranso chifundo okhala m'dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m'dzanja la mnansi wake, ndi m'dzanja la mfumu yake; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m'dzanja mwao sindidzawalanditsa.
7Zef. 3.12; Zek. 11.4, 10, 14; Mat. 11.5M'mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; ina ndinaitcha Chisomo, inzake ndinaitcha Chomanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo.
8Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.
9Pamenepo ndinati, Sindidzadyetsanso inu; chilikufa chife; chosoweka chisoweke; ndi zotsala zidyane, chonse nyama ya chinzake.
10Zek. 11.7Ndipo ndinatenga ndodo yanga Chisomo, ndi kuidula pakati, kuti ndiphwanye pangano langa ndinalichita ndi mitundu yonse ya anthu.
11Zef. 3.12; Mat. 11.5Ndipo linathyoka tsikulo, momwemo zonyankhalala za zoweta, zakundisamalira Ine, zinadziwa kuti ndiwo mau a Yehova.
12Mat. 26.15Ndipo ndinanena nao, Chikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwake masekeli a siliva makumi atatu.
13Mat. 27.9-10Ndipo Yehova anati kwa ine, Kaziponye kwa woumba mbiya, mtengo wake wokometsetsa anandiyesawo. Ndipo ndinatenga masekeli makumi atatu a siliva, ndi kuziponya kwa woumba mbiya, m'nyumba ya Yehova.
14Zek. 11.7Pamenepo ndinadula ndodo yanga ina, ndiyo Chomanganitsa, kuti ndithetse chibale cha pakati pa Yuda ndi Israele.
15 Ezk. 34.2-4 Ndipo Yehova anati kwa ine, Dzitengerenso zipangizo za mbusa wopusa.
16Ezk. 34.2-4Pakuti taonani, ndidzautsa mbusa m'dziko amene sadzazonda otayika, kapena kufunafuna zomwazika, kapena kulunzitsa yothyoka, kapena kudyetsa yamoyo, koma adzadya nyama ya zonenepa, nadzang'amba ziboda zao.
17Yer. 23.1; Yoh. 10.12-13Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga pa dzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.