CHIVUMBULUTSO 16 - Buku Lopatulika Bible 2014

1 Chiv. 14.10 Ndipo ndinamva mau akulu ochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.

2 Eks. 9.9-11; Chiv. 8.7; 13.16 Ndipo anachoka woyamba, natsanulira mbale yake kudziko; ndipo kunakhala chilonda choipa ndi chosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la chilombo nalambira fano lake.

3 Eks. 7.17, 20; Chiv. 8.8-9 Ndipo wachiwiri anatsanulira mbale yake m'nyanja; ndipo kunakhala mwazi ngati wa munthu wakufa; ndipo zamoyo zonse za m'nyanja zidafa.

4 Eks. 7.17, 20; Chiv. 8.8 Ndipo wachitatu anatsanulira mbale yake kumitsinje ndi akasupe a madzi; ndipo kunasanduka mwazi.

5Chiv. 15.3Ndipo ndinamva mngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu, chifukwa mudaweruza kotero;

6Yes. 49.26; Mat. 23.34-35popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.

7Chiv. 15.3Ndipo ndinamva wa pa guwa la nsembe, alinkunena, Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, maweruziro anu ali oona ndi olungama.

8 Chiv. 8.12; 9.17 Ndipo wachinai anatsanulira mbale yake padzuwa; ndipo analipatsa ilo litenthe anthu ndi moto.

9Chiv. 16.11, 21Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalapa kuti amchitire ulemu.

10 Chiv. 9.2; 13.2 Ndipo wachisanu anatsanulira mbale yake pa mpando wachifumu wa chilombo; ndipo ufumu wake unadetsedwa; ndipo anatafuna malilime ao ndi kuwawa kwake,

11Chiv. 16.9, 21nachitira mwano Mulungu wa m'Mwamba chifukwa cha zowawa zao ndi zilonda zao; ndipo sanalapa ntchito zao.

12 Yes. 41.2; Chiv. 9.14 Ndipo wachisanu ndi chimodzi anatsanulira mbale yake pa mtsinje waukulu Yufurate; ndi madzi ake anaphwa, kuti ikonzeke njira ya mafumu ochokera potuluka dzuwa.

13Chiv. 12.3, 9Ndipo ndinaona motuluka m'kamwa mwa chinjoka, ndi m'kamwa mwa chilombo, ndi m'kamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati achule;

141Tim. 4.1; Chiv. 17.14pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.

15Mat. 24.43(Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.)

16Chiv. 19.19Ndipo anawasonkhanitsira kumalo otchedwa m'Chihebri Armagedoni.

17 Chiv. 21.6 Ndipo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mumlengalenga; ndipo m'Kachisimo mudatuluka mau akulu, ochokera kumpando wachifumu ndi kunena, Chachitika;

18Chiv. 6.12; 11.13ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali chivomezi chachikulu chotero sichinaoneke chiyambire anthu padziko, chivomezi cholimba chotero, chachikulu chotero.

19Chiv. 14.18; 17.18; 18.5Ndipo chimudzi chachikulucho chidagawika patatu, ndi midzi ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo wamkali wa mkwiyo wake.

20Chiv. 6.14Ndipo zisumbu zonse zidathawa, ndi mapiri sanapezeka.

21Eks. 9.23-25; Chiv. 11.19; 16.9, 11Ndipo anatsika kumwamba matalala akulu, lonse lolemera ngati talente, nagwa pa anthu; ndipo anthu anachitira Mulungu mwano chifukwa cha mliri wa matalala, pakuti mliri wake ndi waukulu ndithu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help