YOBU 11 - Buku Lopatulika Bible 2014

Zofari adzudzula Yobu pa kudzilungamitsa kwake, namchenjeza alape

1Pamenepo anayankha Zofari wa ku Naama, nati,

2Kodi mau ochulukawa sayenera kuwayankha?

Ndi munthu wa milomo ayenera kuyesedwa wolungama?

3Kodi zotamanda zako ziwatseke anthu pakamwa?

Useka kodi, wopanda munthu wakukuchititsapo manyazi?

4 Yob. 6.10; 10.7 Pakuti unena, Chiphunzitso changa nchoona,

ndipo ndili woyera pamaso pako.

5Koma, ha? Mwenzi atanena Mulungu,

ndi kukutsegulira milomo yake motsutsa;

6 Ezr. 9.13 nakufotokozere zinsinsi za nzeru,

popeza zipindikapindika machitidwe ao!

Chifukwa chake dziwa kuti Mulungu akuiwalira mphulupulu zina.

7 Aro. 11.33; Mas. 145.3 Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa mufunafuna?

Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika?

8Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungachitenji?

Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji?

9Muyeso wake utalikira utali wake wa dziko lapansi,

chitando chake chiposa cha nyanja.

10Akapita, nakatsekera,

nakatulutsa bwalo la mlandu, adzamletsa ndani?

11 Mas. 10.11, 14 Pakuti adziwa anthu opanda pake,

napenyanso mphulupulu, ngakhale saisamalira.

12Koma munthu wopanda pake asowa nzeru,

ngakhale munthu abadwa ngati mwanawabulu.

13Ukakonzeratu mtima wako,

ndi kumtambasulira Iye manja ako;

14 Mas. 101.3 Mukakhala mphulupulu m'dzanja lako, uichotseretu kutali,

ndi chisalungamo chisakhale m'mahema mwako.

15Popeza pamenepo udzakweza nkhope yako opanda banga;

nudzalimbika osachita mantha;

16pakuti udzaiwala chisoni chako,

udzachikumbukira ngati madzi opita.

17Ndipo moyo wako udzayera koposa usana;

kungakhale kuli mdima kudzakhala ngati m'mawa.

18Ndipo udzalimbika mtima popeza pali chiyembekezo;

nudzafunafuna, ndi kugona mosatekeseka.

19Inde udzagona pansi, wopanda wina wakukunjenjemeretsa,

ndipo ambiri adzakupembedza.

20 Lev. 26.16; Miy. 11.7 Koma maso a oipa adzagoma,

ndi pothawirapo padzawasowa,

ndipo chiyembekezo chao ndicho kupereka mzimu wao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help