1Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, mwezi wachitatu, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
2Ezk. 31.18Wobadwa ndi munthu iwe, nena kwa Farao mfumu ya Aejipito ndi aunyinji ake, Ufanana ndi yani m'ukulu wako?
3Dan. 4.10Taona, Asiriya anali mkungudza wa ku Lebanoni ndi nthambi zokoma zovalira, wautali msinkhu, kunsonga kwake ndi kumitambo.
4Madzi anaumeretsa, chigumula chinaukulitsa, mitsinje yake inayenda, nizungulira munda wake, nipititsa michera yake kumitengo yonse ya kuthengoko.
5Dan. 4.11Chifukwa chake msinkhu wake unaposa mitengo yonse ya kuthengo, ndi nthambi zake zinachuluka, ndi nthawi zake zinatalika, chifukwa cha madzi ambiri pophuka uwu.
6Dan. 4.12, 21Mbalame zonse za m'mlengalenga zinamanga zisa zao pa nthambi zake, ndi pansi pa nthawi zake zinaswana nyama zonse za kuthengo, ndi pa mthunzi wake inakhala mitundu yonse yaikulu ya anthu.
7M'mwemo unakoma m'ukulu wake, m'kutalika kwa nthawi zake, popeza muzu wake unakhala kumadzi ambiri.
8Mikungudza ya m'munda wa Mulungu siinathe kuubisa, milombwa siinanga nthambi zake, mifula siinanga nthawi zake; m'munda wa Mulungu munalibe mtengo wofanana nao kukoma kwake.
9Ndinaupanga wokoma ndi nthawi zake zochuluka; ndi mitengo yonse ya m'Edeni inali m'munda wa Mulungu inachita nao nsanje.
10 Dan. 5.20 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mtengowo unakuza msinkhu wake, nufikitsa nsonga yake kumitambo, nukwezeka mtima wake m'kukula kwake,
11ndidzaupereka m'dzanja la wamphamvu wa amitundu; iye adzachita naotu, Ine ndautaya mwa choipa chake.
12Ezk. 28.7Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zake zidagwa pamapiri ndi m'zigwa zonse, ndi nthambi zake zinathyokera ku timitsinje tonse ta m'dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi inatsika kumthunzi wake, niusiya.
13Yes. 18.6Pogwera pake padzakhala mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi nyama zonse za kuthengo zidzakhala pa nthambi zake;
14kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.
15Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija anatsikira kumanda ndinachititsa maliro, ndinamphimbira nyanja, ndinachepsa mitsinje yake, ndi madzi aakulu analetseka; ndipo ndinamdetsera Lebanoni, ndi mitengo yonse ya kuthengo inafota chifukwa cha uwo.
16Ezk. 26.15Ndinagwedeza amitundu ndi phokoso la kugwa kwake, muja ndinagwetsera kumanda, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda; ndi mitengo yonse ya ku Edeni yosankhika, ndi yokometsetsa ya ku Lebanoni, yonse yakumwa madzi, inasangalala munsi mwake mwa dziko lapansi.
17Iwonso anatsika naye kumanda kwa iwo ophedwa ndi lupanga, ndiwo amene adakhala dzanja lake okhala mumthunzi mwake pakati pa amitundu.
18 Ezk. 28.10; 32.19, 21, 24 Momwemo ufanana ndi yani m'ulemerero ndi ukulu pakati pa mitengo ya Edeni? Koma udzatsitsidwa pamodzi ndi mitengo ya Edeni munsi mwake mwa dziko lapansi, udzagona pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Uwu ndi Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.