1 Mas. 40.13-17 Fulumirani kundipulumutsa, Mulungu!
Fulumirani kundithandiza, Yehova.
2Achite manyazi, nadodome
amene afuna moyo wanga.
Abwezedwe m'mbuyo, napepulidwe
amene akonda kundichitira choipa.
3Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi ao
amene akuti, Hede, hede.
4Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu;
nanene kosalekeza iwo akukonda chipulumutso chanu,
abuke Mulungu.
5 Mas. 141.1 Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi;
mundifulumirire, Mulungu.
Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga;
musachedwe, Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.