1 Chiv. 1.13, 16 Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba:
Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolide:
22Ako. 11.13; Chiv. 2.19Ndidziwa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sukhoza kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;
3ndipo uli nacho chipiriro, ndipo walola chifukwa cha dzina langa, wosalema.
4Koma ndili nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya chikondi chako choyamba.
5Mat. 21.41, 43Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikapo nyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.
6Chiv. 2.15Koma ichi uli nacho, kuti udana nazo ntchito za Anikolai, zimene Inenso ndidana nazo.
7Gen. 2.9; Chiv. 2.11, 17, 29Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli m'Paradaiso wa Mulungu.
Kalata wachiwiri, wa kwa Mpingo wa ku Smirina8 Chiv. 1.8, 17-18 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Smirina lemba:
Izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo:
9Yak. 2.5; Chiv. 2.2Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.
10Mat. 24.13; Yak. 1.12Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.
11Chiv. 2.7; 20.14Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene alakika sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.
Kalata wachitatu, wa kwa Mpingo wa ku Pergamo12 Chiv. 1.16 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Pergamo lemba:
Izi anena Iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konsekonse:
13Chiv. 2.9Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.
14Num. 24.14Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.
15Chiv. 2.6Kotero uli nao akugwira chiphunzitso cha Anikolai momwemonso.
162Ate. 2.8Chifukwa chake lapa; ukapanda kutero ndidza kwa iwe posachedwa, ndipo ndidzachita nao nkhondo ndi lupanga la m'kamwa mwanga.
17Yoh. 6.48-50; Chiv. 2.7, 11; 3.12Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wolakika, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pa mwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.
Kalata wachinai, wa kwa Mpingo wa ku Tiatira18 Chiv. 1.14-15 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiatira lemba:
Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira:
19Chiv. 2.2Ndidziwa ntchito zako, ndi chikondi, ndi chikhulupiriro, ndi utumiki, ndi chipiriro chako, ndi kuti ntchito zako zotsiriza zichuluka koposa zoyambazo.
201Maf. 21.25Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.
21Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chigololo chake.
22Taona, ndimponya iye pakama, ndi iwo akuchita chigololo naye kuwalonga m'chisautso chachikulu, ngati salapa iwo ndi kuleka ntchito zake.
23Mas. 26.2; 139.23-24; Mat. 16.27Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.
24Koma ndinena kwa inu, kwa otsala a ku Tiatira, onse amene alibe chiphunzitso ichi, amene sanazindikira zakuya za Satana, monga anena, Sindikusanjikizani katundu wina.
25Chiv. 3.11Koma chimene muli nacho, gwirani kufikira ndikadza.
26Mat. 19.28Ndipo iye amene alakika, ndi iye amene asunga ntchito zanga kufikira chitsiriziro, kwa iye ndidzapatsa ulamuliro wa pa amitundu;
27Mas. 2.8-9ndipo adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo, monga zotengera za woumba mbiya ziphwanyika mapale; monga Inenso ndalandira kwa Atate wanga;
28Chiv. 22.16ndipo ndidzampatsa iye nthanda.
29Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.