YOBU 38 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mulungu aonekera kwa Yobu osamtsutsa. Koma amkumbutsa za ukulu wopambana wa Mulungu. Yobu adzichepetsapo

1 1Maf. 19.11 Pamenepo Yehova anayankha Yobu m'kamvulumvulu, nati,

2 Yob. 34.35 Ndani uyu adetsa uphungu,

ndi mau opanda nzeru?

3Udzimangire m'chuuno tsono ngati mwamuna;

ndikufunsa, undidziwitse.

4 Miy. 8.29 Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi?

Fotokoza ngati udziwa kuzindikira.

5Analemba malire ake ndani, popeza udziwa?

Anayesapo chingwe chake ndani?

6Maziko ake anakumbidwa pa chiyani?

Kapena anaika ndani mwala wake wa pangodya,

7muja nyenyezi za m'mawa zinaimba limodzi mokondwera,

ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?

8 Gen. 1.9 Kapena anatseka nyanja ndani ndi zitseko,

muja idakamula ngati kutuluka m'mimba,

9muja ndinayesa mtambo chovala chake,

ndi mdima wa bii nsalu yake yokulunga,

10ndi kuilembera malire anga,

ndi kuika mipikizo ndi zitseko,

11ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo;

apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?

12Kodi walamulira m'mawa chiyambire masiku ako,

ndi kudziwitsa mbandakucha malo ake;

13kuti agwire malekezero a dziko lapansi,

nakutumule oipa achokeko?

14Lisandulika ngati dothi lonyata pansi pa chosindikiza,

ndi zonse zibuka ngati chovala;

15 Mas. 10.15 ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone,

ndi dzanja losamulidwa lithyoledwa.

16Kodi unalowa magwero a nyanja?

Kodi unayendayenda pozama penipeni?

17Kodi zipata za imfa zinavumbulukira iwe?

Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa?

18Kodi unazindikira chitando cha dziko lapansi?

Fotokozera, ngati uchidziwa chonse.

19Ili kuti njira yomukira pokhala kuunika?

Ndi mdima, pokhala pake pali kuti,

20kuti upite nao kumalire ake,

kuti uzindikire miseu ya kunyumba yake?

21Udziwa, pakuti unabadwa pamenepo,

ndi masiku ako achuluka kuwerenga kwao.

22Kodi unalowa m'zosungiramo chipale chofewa?

Kapena unapenya zosungiramo matalala,

23 Yos. 10.11 amene ndiwasungira tsiku la nsautso,

tsiku lakulimbana nkhondo?

24Njira ili kuti yomukira pogawikana kuunika,

kapena pomwazikira mphepo ya kum'mawa pa dziko lapansi?

25Ndani anachikumbira mchera chimvula,

kapena njira ya bingu la mphezi,

26kuvumbitsa mvula pa dziko lopanda anthu,

kuchipululu kosakhala munthu,

27kukhutitsa thengo la kunkhwangwala,

ndi kuphukitsa msipu?

28 Mas. 147.8; Yer. 14.22 Kodi mvula ili naye atate?

Kapena wabala ndani madontho a mame?

29Chipale chinatuluka m'mimba ya yani?

Ndi chisanu chochokera m'mwamba anachibala ndani?

30Madzi aundana ngati mwala,

ndi pamwamba pa nyanja yozama mpogwirana madzi.

31 Amo. 5.8; Yob. 9.9 Kodi ungamange gulu la Nsangwe?

Kapena kumasula zomangira za Akamwiniatsatana?

32Ungatulutse kodi nyenyezi m'nyengo zao

monga mwa malongosoledwe ao?

Kapena kutsogolera Mlalang'amba ndi ana ake?

33 Yer. 31.35 Kodi udziwa malemba a kuthambo?

Ukhoza kukhazikitsa ufumu wao pa dziko lapansi?

34Kodi udziwa kukwezera mau ako kumitambo,

kuti madzi ochuluka akukute?

35Kodi ukhoza kutumiza mphezi kuti zimuke,

ndi kunena nawe, Tili pano?

36 Mlal. 2.26 Ndani analonga nzeru m'mitambomo?

Ndani waninkha nyenyezi yotsotsoka luntha?

37Adziwa ndani kuwerenga mitambo mwanzeru,

ndi kutsanulira michenje ya kuthambo ndani,

38pokandika fumbi,

ndi kuundana zibuma pamodzi?

39 Mas. 104.21 Kodi ukhoza kusakira mkango waukazi nyama?

Ndi kukwaniritsa chakudya cha misona,

40pamene ibwatama m'ngaka mwao,

nikhala mobisala kulaliramo?

41 Mat. 6.26 Amkonzeratu khungubwi chakudya chake ndani,

pamenepo ana ake afuulira kwa Mulungu,

naulukauluka osowa chakudya?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help