EKSODO 36 - Buku Lopatulika Bible 2014

1Pamenepo anachita Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu aluso, amene Yehova adaika luso ndi nzeru m'mtima mwao adziwe machitidwe ake a ntchito yonse ya utumiki wake wa malo opatulika, monga mwa zonse adauza Yehova.

Amisiri alandira zopereka za anthu

2Ndipo Mose adaitana Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m'mtima mwao, onse ofulumidwa mtima ayandikize kuntchito kuichita.

3Ndipo analandira kwa Mose chopereka chonse, chimene ana a Israele adabwera nacho chikhale cha machitidwe a ntchito ya malo opatulika, aipange nacho. Koma anaonjeza kubwera nazo kwa iye zopereka zaufulu, m'mawa ndi m'mawa.

4Ndipo aluso onse, akuchita ntchito yonse ya malo opatulika, anadza onse ndi kusiya ntchito yao analinkuchita;

52Mbi. 31.10; 2Ako. 8.2-3nanena ndi Mose, ndi kuti, Anthu alinkubwera nazo zochuluka, zakuposera zoyenera ntchito imene Yehova anauza ichitike.

6Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mau mwa chigono chonse, ndi kuti, Asaonjezere ntchito ya ku chopereka cha malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina.

7Popeza zipangizo zinakwanira ntchito yonse ichitike, zinatsalakonso.

Mapangidwe a chihemacho

8Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga Kachisi ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi akerubi, ntchito ya mmisiri.

9Eks. 26Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi mikono inai; nsalu zonse zinafanana muyeso wao.

10Ndipo analumikiza nsalu zisanu ina ndi inzake; nalumikiza nsalu zisanu zina ina ndi inzake.

11Ndipo anaika magango ansalu yamadzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi ku mkawo wa chilumikizano; nachita momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano chachiwiri.

12Anaika magango makumi asanu pa nsalu imodzi, naikanso magango makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; magango anakomanizana lina ndi linzake.

13Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolide, namanga nsalu pamodzi ndi zokowerazo; ndipo Kachisi anakhala mmodzi.

14Ndipo anaomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa Kachisi; anaomba nsalu zophimba khumi ndi imodzi.

15Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wao.

16Ndipo anamanga pamodzi nsalu zisanu pa zokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pa zokha.

17Ndipo anapanga magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo, ya chilumikizano, naika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano china.

18Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi.

19Ndipo anasokera hemalo chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake.

20Ndipo anapanga matabwa a Kachisi, oimirika, a mtengo wakasiya.

21Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwa limodzi ndiko mkono ndi hafu.

22Pa thabwa limodzi panakhala mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; anawapanga momwemo matabwa onse a Kachisi.

23Ndipo anapanga matabwa a Kachisi; matabwa makumi awiri a ku mbali ya kumwera, kumwera;

24napanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri.

25Ndi ku mbali ina ya Kachisi, mbali ya kumpoto, anapanga matabwa makumi awiri, ndi makamwa ao makumi anai asiliva;

26makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.

27Ndi ku mbali ya kumbuyo ya Kachisi kumadzulo anapanga matabwa asanu ndi limodzi.

28Anapanganso matabwa awiri a kungodya za Kachisi, m'mbali zake ziwiri.

29Ndipo anaphatikizika pamodzi patsinde, naphatikizika pamodzi pamutu pake ndi mphete imodzi; anatero nao onse awiri pangodya ziwiri.

30Ndipo panali matabwa asanu ndi atatu. Ndi makamwa ao asiliva, makamwa khumi kudza asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi.

31Ndipo anapanga mitanda ya mtengo wakasiya; isanu ya matabwa a pa mbali ina ya Kachisi,

32ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali inzake ya Kachisi, ndi mitanda isanu ya matabwa a Kachisi ali pa mbali ya kumadzulo.

33Ndipo anapititsa mtanda wa pakatipo, pakati pa matabwa kufikira kuthungo.

34Ndipo anakuta matabwa ndi golide, napanga mphete zao zagolide zikhale zopisamo mitandayo, nakuta mitandayo ndi golide.

35Ndipo anaomba nsalu yotchinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anachiomba ndi akerubi ntchito ya mmisiri.

36Ndipo anaipangira mizati inai ya kasiya, nazikuta ndi golide; zokowera zao zinali zagolide; ndipo anaziyengera makamwa anai asiliva.

37Ndipo anaomba nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula;

38ndi nsanamira zake zisanu ndi zokowera zao; nakuta mitu yao ndi mitanda yao ndi golide; ndi makamwa ao asanu anali amkuwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help