1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Akaima mkazi, nakabala mwana wamwamuna, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; monga masiku ake akukhala padera, podwala iye, adzakhala wodetsedwa.
3Gen. 17.12; Luk. 1.59; 2.21Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adule khungu la mwanayo.
4Ndipo akhale m'mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi atatu kudza atatu; asakhudze kanthu kopatulika, kapena kulowa m'malo opatulika, kufikira adakwanira masiku a kumyeretsa kwake.
5Koma akabala mwana wamkazi, akhale wodetsedwa masabata awiri, monga umo amakhala padera; ndipo adzakhala m'mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi.
6Ndipo atakwanira masiku a kumyeretsa kwake pa mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, adze naye mwanawankhosa wa chaka chimodzi ikhale nsembe yopsereza, ndi bunda, kapena njiwa zikhale nsembe yauchimo, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe;
7ndipo iye abwere nayo pamaso pa Yehova, namchitire chomtetezera mkaziyo, ndipo adzakhala woyeretsedwa wochira kukha mwazi kwake.
8Luk. 2.24Ichi ndi chilamulo cha kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala woyera.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.