1Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse;
ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
2 1Maf. 8.28, 30; Yes. 42.21 Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera,
ndi kuyamika dzina lanu,
chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu;
popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.
3Tsiku loitana ine, munandiyankha,
munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga.
4 Mas. 102.15, 22 Mafumu onse a pa dziko lapansi adzakuyamikani,
Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu.
5Ndipo adzaimbira njira za Yehova;
pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.
6 Yak. 4.6 Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo;
koma wodzikuza amdziwira kutali.
7 Mas. 23.3-4 Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo;
mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu,
ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
8 Afi. 1.6 Yehova adzanditsirizira za kwa ine:
Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse:
Musasiye ntchito za manja anu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.