1
phindu lake liposa golide woyengeka.
15 Mat. 13.44 Mtengo wake uposa ngale;
ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.
16Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake;
chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere.
17Njira zake zili zokondweretsa,
mayendedwe ake onse ndiwo mtendere.
18 Gen. 2.9; 3.22 Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira;
wakuiumirira ngwodala.
19Yehova anakhazika dziko ndi nzeru;
naika zamwamba ndi luntha.
20Zakuya zinang'ambika ndi kudziwa kwake;
thambo ligwetsa mame.
21Mwananga, zisachokere kumaso ako;
sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira;
22ndipo mtima wako udzatengapo moyo,
ndi khosi lako chisomo.
23 Mas. 91.11-12 Pompo udzayenda m'njira yako osaopa,
osaphunthwa phazi lako.
24 Lev. 26.6 Ukagona, sudzachita mantha;
udzagona tulo tokondweretsa.
25 Mas. 91.5 Usaope zoopsa zodzidzimutsa,
ngakhale zikadza zopasula oipa;
26pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako,
nadzasunga phazi lako lingakodwe.
Malangizo ena osiyana27 Aro. 13.7; Agal. 6.10 Oyenera kulandira zabwino usawamane;
pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.
28 Lev. 19.13 Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso,
ndipo mawa ndidzakupatsa;
pokhala uli nako kanthu.
29Usapangire mnzako chiwembu;
popeza akhala nawe pafupi osatekeseka.
30 Aro. 12.18 Usakangane ndi munthu chabe,
ngati sanakuchitire choipa.
31Usachitire nsanje munthu wachiwawa;
usasankhe njira yake iliyonse.
32 Mas. 25.14 Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova;
koma chinsinsi chake chili ndi oongoka.
33 Zek. 4.3, 4 Yehova atemberera za m'nyumba ya woipa;
koma adalitsa mokhalamo olungama.
34 1Pet. 5.5 Anyozadi akunyoza,
koma apatsa akufatsa chisomo.
35Anzeru adzalandira ulemu cholowa chao;
koma opusa adzakweza manyazi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.