MASALIMO 36 - Buku Lopatulika Bible 2014

Kuipitsitsa kwa anthu, kukometsetsa kwa MulunguKwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.

1 Aro. 3.18 Cholakwa cha woipayo chimati m'kati mwa mtima wanga,

palibe kuopa Mulungu pamaso pake.

2Pakuti adzidyoletsa yekha m'kuona kwake,

kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.

3Mau a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga,

waleka kuzindikira ndi kuchita bwino.

4Alingirira zopanda pake pakama pake;

adziika panjira posati pabwino;

choipa saipidwa nacho.

5 Mas. 57.10 Yehova, m'mwamba muli chifundo chanu;

choonadi chanu chifikira kuthambo.

6Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu;

maweruzo anu akunga chozama chachikulu,

Yehova, musunga munthu ndi nyama.

7 Rut. 2.12; Mas. 91.4 Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi!

Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu.

8 Mas. 65.4 Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu,

ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.

9 Yer. 2.13; Yoh. 1.9; 4.10, 14 Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu,

M'kuunika kwanu tidzaona kuunika.

10 Yer. 22.16 Tanimphitsani chifundo chanu pa iwo akudziwa Inu;

ndi chilungamo chanu pa oongoka mtima.

11Phazi la akudzikuza lisandifikire ine,

ndi dzanja la oipa lisandichotse.

12Pomwepo padagwera ochita zopanda pake.

Anawalikha, ndipo sadzatha kuukanso.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help