YESAYA 24 - Buku Lopatulika Bible 2014

Chilango cha Mulungu cha pa dziko la Israele, ndi pa dziko lonse lapansi

1Taonani, Yehova apululutsa dziko, nalipasula, nalitembenuza dodolido, nabalalitsa okhalamo ake.

2Ezk. 7.12-13; Hos. 4.9Ndipo padzakhala monga ndi anthu, moteronso ndi ansembe; monga ndi mtumiki, moteronso ndi mbuyake; monga ndi mdzakazi, moteronso ndi mbuyake wamkazi; monga ndi wogula, moteronso ndi wogulitsa; monga ndi wobwereka, moteronso ndi wombwereka; monga ndi wotenga phindu, moteronso ndi wombwezera phindu kwa iye.

3Dziko lidzapululuka konse, ndi kupasulidwa ndithu; pakuti Yehova anenana mau amenewa.

4Dziko lirira nilifota, dziko lilefuka nilifota, anthu omveka a padziko alefuka.

5Gen. 3.17Dzikonso laipitsidwa ndi okhalamo ake omwe, chifukwa iwo alakwa pamalamulo nasinthanitsa malemba, nathyola chipangano cha nthawi zonse.

6Mala. 4.6Chifukwa chake chitemberero chadya dziko, ndi amene akhala m'menemo apezedwa ochimwa, chifukwa chake okhalamo a padziko atenthedwa, ndipo anthu owerengeka atsala.

7Vinyo watsopano alira, mpesa ulefuka, mitima yonse yokondwa iusa moyo.

8Yer. 7.34; Chiv. 18.22Kusangalala kwa mangaka kwalekeka, phokoso la iwo amene asekera litha, kukondwa kwa mngoli kwalekeka.

9Iwo sadzamwa vinyo ndi kuimba nyimbo; chakumwa chaukali chidzawawa kwa iwo amene achimwa.

10Mudzi wosokonezeka wagwetsedwa pansi; nyumba zonse zatsekedwa, kuti asalowemo munthu.

11Muli mfuu m'makwalala chifukwa cha vinyo; kukondwa konse kwadetsedwa, kusangalala kwa dziko kwatha.

12M'mudzi mwatsala bwinja, ndi chipata chamenyedwa ndi chipasuko.

13Yes. 17.5-6Chifukwa chake padzakhala chotero pakati pa dziko mwa anthu, ngati kugwedeza kwa mtengo wa azitona, ngati khunkha la mphesa, pakutha masika ake.

14Amenewa adzakweza mau ao, nadzafuula; chifukwa cha chifumu cha Yehova, iwo adzafuula zolimba panyanja.

15Chifukwa chake lemekezani inu Yehova kum'mawa, ngakhale dzina la Yehova, Mulungu wa Israele, m'zisumbu za m'nyanja.

16 Yer. 5.11 Kuchokera ku malekezero a dziko ife tamva nyimbo zolemekeza wolungama. Koma ine ndinati, Ndaonda ine, ndaonda ine, tsoka kwa Ine! Amalonda onyenga amangonyenga; inde ogulitsa onyenga apambana kunyenga.

17Amo. 5.19Mantha ndi dzenje ndi msampha zili pa iwe, wokhala m'dziko.

18Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsa, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka.

19Yer. 4.23Dziko lapansi lasweka ndithu, dziko lapansi lasungunukadi, dziko lapansi lili kugwedezeka kopambana.

20Dziko lapansi lidzachita dzandidzandi, ngati munthu woledzera, ndi kunjenjemera, ngati chilindo; ndi kulakwa kwake kudzalilemera, ndipo lidzagwa losaukanso.

21Ndipo padzali tsiku limenelo, kuti Yehova adzazonda kumwamba khamu lakumwamba, ndi mafumu a dziko lapansi.

22Ndipo iwo adzasonkhanitsidwa pamodzi, monga ndende zimasonkhanitsidwa m'dzenje, ndi kutsekeredwa m'kaidi, ndipo atapita masiku ambiri adzawazonda.

23Yow. 2.31; Chiv. 19.4-6Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi m'Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help