EZEKIELE 39 - Buku Lopatulika Bible 2014

1Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, nenera motsutsana naye Gogi, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Gogi, iwe mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala;

2ndipo ndidzakutembenuza, ndi kukutsogolera, ndi kukweza iwe uchoke ku malekezero a kumpoto; ndipo ndidzadza nawe kumapiri a Israele;

3ndipo ndidzakantha uta wako kuuchotsa m'dzanja lako lamanzere, ndi kutayitsa mivi yako kudzanja lako lamanja.

4Udzagwa pa mapiri a Israele, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zilombo za kuthengo, akuyese chakudya.

5Udzagwa kuthengo, koyera, pakuti ndanena ndine, ati Ambuye Yehova.

6Amo. 1.4Ndipo ndidzatumizira moto Magogi, ndi iwo okhala mosatekeseka m'zisumbu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

7Lev. 18.21Ndipo ndidzadziwikitsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Israele, osalola dzina langa loyera aliipsenso; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Woyerayo wa Israele.

8Chiv. 16.17; 21.6Taonani, chikudza, chidzachitika, ati Ambuye Yehova, ndilo tsiku ndanenalo.

9Ndipo iwo okhala m'midzi ya Israele adzatuluka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zotchinjiriza, mauta, ndi mivi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri;

10osatenga nkhuni kuthengo, kapena kuzitema kunkhalango; popeza adzasonkha moto ndi zidazo; nadzafunkha iwo amene anawafunkha, ndi kulanda zao za iwo adalanda zaozo, ati Ambuye Yehova.

11Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzapatsa Gogi manda m'Israele, chigwa cha opitawo kum'mawa kwa nyanja; ndipo lidzaletsa opitawo, ndipo adzaika komweko Gogi ndi unyinji wake wonse, nadzachitcha, Chigwa cha unyinji wa Gogi.

12Deut. 21.23Ndi a nyumba ya Israele adzapititsa miyezi isanu ndi iwiri alikuwaika, kuti ayeretse dziko.

13Inde anthu onse a m'dziko adzawaika, nadzamveka nako tsiku lakulemekezedwa Ine, ati Ambuye Yehova.

14Ndipo adzasankha anthu akupitapitabe m'dziko, ndi pamodzi ndi opitapitawo anthu akuika mafupa otsala pamtunda, kuliyeretsa; pakutha miyezi isanu ndi iwiri adzapwaira.

15Ndipo opitapitawo adzapitapita m'dziko, ndipo wina akaona fupa la munthu aikepo chizindikiro, mpaka oikawo aliika m'chigwa cha unyinji wa Gogi.

16Ndipo dzina la mudzi lidzakhala Hamona. Momwemo adzayeretsa dziko.

17 Chiv. 19.17-18 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova, Nena kwa mbalame za mitundu yonse, ndi kwa nyama zonse za kuthengo, Memezanani, idzani, sonkhanani kumbali zonse, kudza kunsembe yanga imene ndikupherani, ndiyo nsembe yaikulu pa mapiri a Israele, kuti mudzadye nyama ndi kumwa mwazi.

18Chiv. 19.17-18Mudzadya nyama ya amphamvu, ndi kumwa mwazi wa akalonga a padziko, wa nkhosa zamphongo, wa anaankhosa, ndi wa mbuzi, ndi wa ng'ombe, zonsezi zonenepa za ku Basani.

19Ndipo mudzadya zonona mpaka mudzakhuta, ndi kumwa mwazi mpaka mudzaledzera za nsembe yanga ndakupherani.

20Ndipo podyera panga mudzakhuta akavalo, ndi magaleta, ndi anthu amphamvu, ndi anthu onse a nkhondo, ati Ambuye Yehova.

21Ezk. 38.16Ndipo ndidzaika ulemerero wanga mwa amitundu; ndi amitundu onse adzaona chiweruzo changa ndachichita, ndi dzanja langa limene ndinawaikira.

22Yow. 2.27Ndipo nyumba ya Israele idzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, kuyambira tsiku ilo ndi m'tsogolomo.

23Deut. 31.17; Ezk. 36.18-23Ndipo amitundu adzadziwa kuti nyumba ya Israele idalowa undende chifukwa cha mphulupulu zao, popeza anandilakwira Ine; ndipo ndinawabisira nkhope yanga; m'mwemo ndinawapereka m'dzanja la adani ao, nagwa iwo onse ndi lupanga.

24Ndinachita nao monga mwa kudetsedwa kwao, ndi monga mwa kulakwa kwao, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.

25 Yer. 30.3, 18 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsopano ndidzabweza undende wa Yakobo, ndi kuchitira chifundo nyumba yonse ya Israele, ndipo ndidzachitira dzina langa loyera nsanje.

26Dan. 9.16Ndipo adzasenza manyazi ao, ndi zolakwa zao zonse, zimene anandilakwira nazo, pokhala mosatekeseka iwo m'dziko lao, opanda wina wakuwaopsa;

27nditabwera nao kuchoka kwa mitundu ya anthu, nditawasokolotsa m'maiko a adani ao, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa iwo pamaso pa amitundu ambiri.

28Ezk. 39.22Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, popeza ndinalola atengedwe ndende kunka kwa amitundu, koma ndinawasonkhanitsanso akhale m'dziko lao, osasiyakonso mmodzi yense wa iwowa.

29Yes. 54.8; Yow. 2.28; Zek. 12.10; Mac. 2.17Ndipo sindidzawabisiranso nkhope yanga, popeza ndatsanulira mzimu wanga pa nyumba ya Israele, ati Ambuye Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help