1 Yes. 29.11; Ezk. 2.9-10 Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.
2Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu wakulalikira ndi mau akulu, Ayenera ndani kutsegula buku, ndi kumasula zizindikiro zake?
3Ndipo sanathe mmodzi m'Mwamba, kapena padziko, kapena pansi pa dziko kutsegula pabukupo, kapena kulipenya.
4Ndipo ndinalira kwambiri, chifukwa sanapezedwa mmodzi woyenera kutsegula bukulo, kapena kulipenya;
5Gen. 49.9-10; Yes. 11.1, 10; Aheb. 7.14ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, walakika kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.
6Yes. 53.7; Yoh. 1.29, 36; Chiv. 4.5Ndipo ndinaona pakati pa mpando wachifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akulu, Mwanawankhosa ali chilili ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m'dziko lonse.
7Chiv. 4.2Ndipo anadza, nalitenga kudzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu.
8Mas. 141.2; Chiv. 4.8, 10Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.
9Mac. 20.28; Akol. 1.14; Chiv. 4.11; 7.9Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,
10ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.
11Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva mau a angelo ambiri pozinga mpando wachifumu, ndi zamoyo ndi akulu; ndipo mawerengedwe ao anali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi zikwi za zikwi;
12Chiv. 4.11akunena ndi mau akulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko.
13Afi. 2.10; 1Pet. 4.11Ndipo cholengedwa chilichonse chili m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi pa dziko, ndi m'nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, kufikira nthawi za nthawi.
14Ndipo zamoyo zinai zinati, Amen. Ndipo akuluwo anagwa pansi nalambira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.