1Elihu anabwereza, nati,
2Mundilole pang'ono, ndidzakuuzani,
pakuti ndili naonso mau akunenera Mulungu.
3Ndidzatenga nzeru zanga kutali,
ndidzavomereza kuti Mlengi wanga ndi wolungama.
4Pakuti zoonadi, mau anga sali abodza,
wakudziwitsa mwangwiro ali nanu.
5Taonani, Mulungu ndiye mwini mphamvu,
ndipo sapeputsa munthu;
mphamvu ya nzeru zake ndi yaikulu.
6Sasunga woipa akhale ndi moyo,
koma awaninkha ozunzika zowayenera iwo.
7 Mas. 33.18 Sawachotsera wolungama maso ake,
koma pamodzi ndi mafumu pa mpando wao
awakhazika chikhazikire, ndipo akwezeka.
8Ndipo akamangidwa m'nsinga,
nakakodwa ndi zingwe za mazunzo,
9pamenepo awafotokozera ntchito zao,
ndi zolakwa zao, kuti anachita modzikuza.
10Awatseguliranso m'khutu mwao kuti awalangize,
nawauza abwerere kuleka mphulupulu.
11 Yes. 1.19-20 Akamvera ndi kumtumikira,
adzatsiriza masiku ao modala,
ndi zaka zao mokondwera.
12Koma akapanda kumvera adzatayika ndi lupanga,
nadzatsirizika osadziwa kanthu.
13 Aro. 2.5 Koma iwo a mtima wakunyoza Mulungu, akundika mkwiyo,
akawamanga Iye, safuulira.
14Iwowa akufa akali biriwiri,
ndi moyo wao utayika ngati odetsedwa.
15Apulumutsa wozunzika mwa kuzunzika kwake,
nawatsegulira m'khutu mwao mwa kupsinjika kwao.
16Inde akadakukopani muchoke posaukira,
mulowe kuchitando kopanda chopsinja;
ndipo zoikidwa pagome panu zikadakhala zonona ndithu.
17Koma mukadzazidwa nazo zolingirira oipa,
zolingirirazo ndi chiweruzo zidzakugwiranibe.
18Pakuti muchenjere, mkwiyo ungakunyengeni muchite mnyozo;
ndipo usakusokeretseni ukulu wa dipoli.
19Chuma chanu chidzafikira kodi, kuti simudzakhala wopsinjika,
kapena mphamvu yanu yonse yolimba?
20Musakhumbe usiku,
umene anthu alikhidwe m'malo mwao.
21 Aheb. 11.24-25 Chenjerani, musalunjike kumphulupulu;
pakuti mwaisankha iyi mutazunzidwa.
22 1Ako. 2.16 Taonani, Mulungu achita mokwezeka mu mphamvu yake,
mphunzitsi wakunga Iye ndani?
23Anamuikira njira yake ndani?
Adzati ndani, Mwachita chosalungama?
24 Mas. 92.4-5 Kumbukirani kuti mukuze ntchito zake
zimene anaziimbira anthu.
25Anthu onse azipenyerera,
anthu aziyang'anira kutali.
26 1Ako. 13.12 Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa;
chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.
27Pakuti akweza madontho a mvula,
akhetsa mvula ya m'nkhungu yake
28Imene mitambo itsanulira,
nivumbitsira anthu mochuluka.
29Pali munthu kodi wodziwitsa mayalidwe a mitambo,
ndi kugunda kwa msasa wake?
30Taonani, Iye ayala kuunika kwake pamenepo.
Navundikira kunsi kwake kwa nyanja.
31 Mas. 136.25; Mac. 14.17 Pakuti aweruza nazo mitundu ya anthu
apatsa chakudya chochuluka.
32Akutidwa manja ake ndi mphezi,
nailamulira igwere pofunapo Iye.
33Kugunda kwake kulalikira za Iye,
zoweta zomwe zilota mtambo woyandikira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.