MASALIMO 127 - Buku Lopatulika Bible 2014

Madalitso onse, a m'banja omwe, achokera kwa MulunguNyimbo yokwerera; ya Solomoni.

1 Mas. 121.3-5 Akapanda kumanga nyumba Yehova,

akuimanga agwiritsa ntchito chabe;

akapanda kusunga mudzi Yehova,

mlonda adikira chabe.

2 Gen. 3.17, 19 Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo,

kudya mkate wosautsa kuupeza;

kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.

3 Gen. 33.5; Yos. 24.3 Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova;

chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.

4Ana a ubwana wake wa munthu

akunga mivi m'dzanja lake la chiphona.

5 Miy. 27.11 Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake:

sadzachita manyazi iwo,

pakulankhula nao adani kuchipata.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help