1 2Ate. 2.3; 2Tim. 3.13; 2Pet. 2.1 Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda,
2Mat. 7.15m'maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olochedwa m'chikumbu mtima mwao monga ndi chitsulo chamoto;
3Aro. 14.3, 6, 17; 1Ako. 7.28a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.
4Aro. 14.14, 20Pakuti cholengedwa chonse cha Mulungu nchabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi chiyamiko;
5pakuti kayeretsedwa ndi Mau a Mulungu ndi kupemphera.
A utumiki akhale okhulupirika ndi achangu6 2Tim. 3.14-15 Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa m'mauwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;
7koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kuchita chipembedzo;
8Mat. 6.33; 19.29; Akol. 2.23; 1Tim. 6.6pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.
9Okhulupirika mauwa ndi oyenera kulandiridwa konse.
101Ako. 4.11-12Pakuti kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirira.
11Lamulira izi, nuziphunzitse.
121Ako. 16.11; Tit. 2.7Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.
13Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kuchenjeza, kulangiza.
14Mac. 19.6; 2Tim. 1.6Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu.
15Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.
16Mac. 20.28Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.