1 Yow. 1.15; Oba. 15 Muombe lipenga m'Ziyoni, nimufuulitse m'phiri langa lopatulika; onse okhala m'dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lilinkudza, pakuti liyandikira;
2Amo. 5.18, 20tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m'mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.
3Moto unyambita pamaso pao, ndi m'mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m'mbuyo mwao likunga chipululu chopanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka.
4Chiv. 9.7-9Maonekedwe ao aoneka ngati akavalo, nathamanga ngati akavalo a nkhondo.
5Atumphako ngati mkokomo wa magaleta pamwamba pa mapiri, ngati kulilima kwa malawi a moto akupsereza ziputu, ngati mtundu wamphamvu wa anthu ondandalikira nkhondo.
6Pamaso pao mitundu ya anthu ikumva zowawa, nkhope yonse zitumbuluka.
7Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda lililonse njira yake, osasokonezeka m'mabande ao.
8Sakankhana, ayenda lililonse m'mopita mwake; akagwa m'zida, siithyoka nkhondo yao.
9Alumphira mudzi, athamanga palinga, akwerera nyumba, alowera pamazenera ngati khungu.
10Yes. 13.10; Mat. 24.29Dziko lapansi linjenjemera pamaso pao, thambo ligwedezeka, dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao;
11Yow. 1.15ndipo Yehova amveketsa mau ake pamaso pa khamu lake la nkhondo; pakuti a m'chigono mwake ndi ambirimbiri; pakuti Iye wakuchita mau ake ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikulu ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?
12Hos. 12.6Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kuchita maliro;
13Mas. 51.17; 86.5, 15; Hos. 12.6ndipo ng'ambani mitima yanu, si zovala zanu ai; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima, ndi woleka choipacho.
142Sam. 12.22; 3.9Kaya, Yona kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.
15 Yow. 1.14 Ombani lipenga m'Ziyoni, patulani tsiku losala, lalikirani msonkhano woletsa,
16Eks. 19.10, 22sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati atuluke m'chipinda mwake, ndi mkwatibwi m'mogona mwake.
17Eks. 32.11-12; Mas. 42.10Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?
Lonjezo lakuti chidzachuluka chakudya18 Zek. 1.14 Pamenepo Yehova anachitira dziko lake nsanje, nachitira anthu ake chifundo.
19Yow. 1.10; Mala. 3.10-12Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ake, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale chitonzo mwa amitundu;
20koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu.
21Usaopa, dziko iwe; kondwera, nusekerere; pakuti Yehova wachita zazikulu.
22Yow. 1.18-20Musamaopa, nyama zakuthengo inu; pakuti m'chipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.
23Mas. 101.1, 2; Hab. 3.18; Yak. 5.7Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere m'Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula ya chizimalupsa, monga mwa chilungamo chake; nakuvumbitsirani mvula, mvula ya chizimalupsa ndi ya masika mwezi woyamba.
24Ndipo madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m'zosungiramo zao.
25Yow. 1.4Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi chirimamine, ndi anoni, ndi chimbalanga, gulu langa lalikulu la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu.
26Ndipo mudzadyaidya ndi kukhuta, nimudzalemekeza dzina la Yehova Mulungu wanu, amene anachita nanu modabwitsa; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse.
27Yow. 3.17Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndili pakati pa Israele, ndi kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, palibe wina; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse.
28 Mac. 2.17-21; Yes. 32.15 Ndipo kudzachitika m'tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;
29ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo.
30Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa kuthambo ndi pa dziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo.
31Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.
32Ndipo kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa; pakuti m'phiri la Ziyoni ndi m'Yerusalemu mudzakhala chipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehova adzawaitana.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.