1 Mas. 85.2-3; Aro. 4.6-8 Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake;
wokwiriridwa choipa chake.
2 Yob. 1.7 Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zake;
ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo.
3Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba
ndi kubuula kwanga tsiku lonse.
4 1Sam. 5.6-7 Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine;
uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.
5 Luk. 15.18, 21; 1Yoh. 1.9 Ndinavomera choipa changa kwa Inu;
ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa.
Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga;
ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.
6 Mas. 69.1; Yes. 55.6 Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu,
pa nthawi ya kupeza Inu;
indetu pakusefuka madzi aakulu
sadzamfikira iye.
7 Eks. 15.1-18; Ower. 5.1-31; Mas. 119.114 Inu ndinu mobisalira mwanga;
m'nsautso mudzandisunga;
mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.
8 Mas. 25.4 Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo;
ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
9 Miy. 26.3; Yak. 3.3 Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru;
zomangira zao ndizo cham'kamwa ndi chapamutu zakuwakokera,
pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.
10 Miy. 13.21; Yer. 17.7; Aro. 2.9 Zisoni zambiri zigwera woipa;
koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.
11 Mas. 64.10 Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima;
ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.