1
nalingiriranji anthu zopanda pake?
2Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi,
nachita upo akulu pamodzi,
Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,
3 Luk. 19.14 Tidule zomangira zao,
titaye nsinga zao.
4 Miy. 1.8 Wokhala m'mwambayo adzaseka;
Ambuye adzawanyoza.
5Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wake,
nadzawaopsa m'ukali wake.
6Koma Ine ndadzoza mfumu yanga
Pa Ziyoni, phiri langa loyera.
7 Mac. 13.33; Aheb. 1.5 Ndidzauza za chitsimikizo:
Yehova ananena ndi Ine,
Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala.
8 Mas. 72.8 Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu
akhale cholowa chako,
ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako.
9 Chiv. 2.27 Udzawathyola ndi ndodo yachitsulo;
udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.
10Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru;
langikani, oweruza inu a dziko lapansi.
11 Aheb. 12.28 Tumikirani Yehova ndi mantha,
ndipo kondwerani ndi chinthenthe.
12 Mas. 34.8; Yer. 17.7; Yoh. 5.23; Aro. 9.33 Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye,
ndipo mungatayike m'njira
ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake.
Odala onse akumkhulupirira Iye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.