YOBU 32 - Buku Lopatulika Bible 2014

Elihu adzudzula Yobu ndi mabwenzi atatu omwe

1Pamenepo amuna atatuwa analeka kumyankha Yobu; pakuti anali wolungama pamaso pake pa iye mwini.

2Ndipo adapsa mtima Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi, wa chibale cha Ramu, adapsa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.

3Adapsa mtima pa mabwenzi ake atatu omwe, pakuti anasowa pomyankha; koma anamtsutsa Yobu kuti ali woipa.

4Ndipo Elihu analindira kulankhula ndi Yobu, popeza akulu misinkhu ndi iwowa.

5Koma pakuona Elihu kuti anthu atatuwa anasowa poyankha pakamwa pao anapsa mtima.

6Ndipo Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi anayankha, nati,

Ine ndine mnyamata, inu ndinu okalamba;

chifukwa chake ndinadziletsa,

ndi kuopa kukuonetsani monga umo ndayesera ine.

7Ndinati, Amisinkhu anene,

ndi a zaka zochuluka alangize nzeru.

8 Gen. 2.7; 1Maf. 2.12; Yak. 1.5 Koma m'munthu muli mzimu,

ndi mpweya wa Wamphamvuyonse wawazindikiritsa.

9 1Ako. 1.26-27 Akulu sindiwo eni nzeru,

ndi okalamba sindiwo ozindikira chiweruzo.

10Chifukwa chake ndinati, Ndimvereni ine,

inenso ndidzaonetsa monga umo ndayesera ine.

11Taonani, ndinalindira mau anu,

ndinatcherera khutu zifukwa zanu,

pofunafuna inu ponena.

12Inde ndinasamalira inu;

koma taonani, panalibe womtsutsa Yobu,

kapena wakumbwezera mau pakati pa inu.

13Msamati, Tapeza nzeru ndife,

Mulungu akhoza kumkhulula, si munthu ai;

14popeza sanandiponyere ine mau,

sindidzamyankha ndi maneno anu.

15Asumwa, sayankhanso, Anawathera mau.

16Kodi ndidzangolindira popeza sanena iwo,

popeza akhala duu osayankhanso?

17Ndidzayankha inenso mau anga,

ndidzaonetsa inenso za m'mtima mwanga.

18Pakuti ndadzazidwa ndi mau,

ndi mzimu wa m'kati mwanga undifulumiza.

19Taonani, m'chifuwa mwanga muli ngati vinyo

wosowa popungulira,

ngati matumba atsopano akuti aphulike.

20Ndidzanena kuti chifundo chitsike;

ndidzatsegula milomo yanga ndi kuyankha.

21 Miy. 24.23; Mat. 22.16 Ndisati ndisamalire nkhope ya munthu,

kapena kumtchula munthu maina omdyola nao;

22pakuti sindidziwa kutchula maina osyasyalika;

ndikatero Mlengi wanga adzandichotsa msanga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help