1 Mas. 83.1 Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira;
thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva;
pakuti ngati munditontholera ine,
ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
2 1Maf. 8.22, 28-29 Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu,
pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.
3Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa,
ndi ochita zopanda pake;
amene alankhula zamtendere ndi anansi ao,
koma mumtima mwao muli choipa.
4 2Tim. 4.14 Muwapatse monga mwa ntchito zao,
ndi monga mwa choipa chochita iwo;
muwapatse monga mwa machitidwe a manja ao;
muwabwezere zoyenera iwo.
5 Yes. 5.12 Pakuti sasamala ntchito za Yehova,
kapena machitidwe a manja ake,
adzawapasula, osawamanganso.
6Wodalitsika Yehova, Pakuti adamva mau a kupemba kwanga.
7 Mas. 3.3 Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa;
mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza,
chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu;
ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.
8Yehova ndiye mphamvu yao,
inde mphamvu ya chipulumutso cha wodzozedwa wake.
9 Mas. 78.71 Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholandira chanu;
muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.