YONA 4 - Buku Lopatulika Bible 2014

Kudandaula kwa Yona, kumdzudzula kwa Mulungu

1Koma sikudakomera Yona konse, ndipo anapsa mtima.

2Eks. 34.6; Mas. 86.5; Yow. 2.13Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.

31Maf. 19.4Ndipo tsopano, Yehova, mundichotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai.

4Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi?

5Pamenepo Yona anatuluka m'mudzi, nakhala pansi kum'mawa kwa mudzi, nadzimangira komweko thandala, nakhala pansi pake mumthunzi mpaka adzaona chochitikira mudzi.

6Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake, kumlanditsa m'nsautso yake. Ndipo Yona anakondwera kwambiri chifukwa cha msatsiwo.

7Koma Mulungu anauikira mphanzi pakucha m'mawa mwake, ndiyo inadya msatsi, nufota.

8Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.

9Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.

10Ndipo Yehova anati, Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirapo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;

11ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mudzi waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help