MASALIMO 122 - Buku Lopatulika Bible 2014

Apempherera mtendere wa YerusalemuNyimbo yokwerera; ya Davide.

1

3Yerusalemu anamangidwa

ngati mudzi woundana bwino:

4 Deut. 16.16 Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova;

akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova.

5 2Mbi. 19.8 Pakuti pamenepo anaika mipando ya chiweruzo,

mipando ya nyumba ya Davide.

6 Yer. 29.7 Mupempherere mtendere wa Yerusalemu;

akukonda inu adzaona phindu.

7M'linga mwako mukhale mtendere,

m'nyumba za mafumu mukhale phindu.

8Chifukwa cha abale anga ndi mabwenzi anga,

ndidzanena tsopano, Mukhale mtendere mwa inu.

9 Neh. 2.10 Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathu

ndidzakufunira zokoma.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help