MASALIMO 62 - Buku Lopatulika Bible 2014

Posautsidwa Davide athamangira Mulungu yekhaKwa Mkulu wa Nyimbo, pa Yedutuni, Salimo la Davide.

1 Mas. 33.20 Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha;

chipulumutso changa chifuma kwa Iye.

2 Mas. 18.2 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;

msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.

3Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti,

kumupha iye, nonsenu,

monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?

4 Mas. 28.3 Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake;

akondwera nao mabodza;

adalitsa ndi m'kamwa mwao,

koma atemberera mumtima.

5Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha;

pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye.

6Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa,

msanje wanga, sindidzagwedezeka.

7 Yer. 3.23 Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga.

Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.

8 1Sam. 1.15; Mas. 42.4 Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu,

tsanulirani mitima yanu pamaso pake.

Mulungu ndiye pothawirapo ife.

9 Yes. 40.15, 17 Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu akulu ndi bodza,

pakuwayesa apepuka;

onse pamodzi apepuka koposa mpweya.

10 Luk. 12.15 Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba;

chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.

11 Chiv. 19.1 Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri,

kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu.

12 Mas. 103.8; Miy. 24.12; Yer. 32.19; Mat. 16.27; Aef. 6.8; Akol. 3.25 Chifundonso ndi chanu, Ambuye,

Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense

monga mwa ntchito yake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help